Yobu 15
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mawu a Elifazi
15 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
2 “Kodi munthu wanzeru angayankhe ndi mawu achabechabe otere,
kapena angakhutitse mimba yake ndi mphepo yotentha yochokera kummawa?
3 Kodi angathe kutsutsa ndi mawu opanda pake,
kapena kuyankhula mawu opanda phindu?
4 Koma iwe ukuchepetsa zoopa Mulungu
ndipo ukutchinga zodzikhuthulira kwa Mulungu.
5 Tchimo lako ndiye likuyankhulitsa pakamwa pakopo;
ndipo watengera mayankhulidwe a atambwali.
6 Pakamwa pakopo ndiye pakukutsutsa osati pakamwa panga;
milomo yakoyo ikukutsutsa.
7 “Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa?
Kodi unalengedwa mapiri asanalengedwe?
8 Kodi unali mʼgulu la alangizi a Mulungu?
Kodi ukudziyesa wanzeru ndiwe wekha?
9 Kodi iwe umadziwa chiyani chimene ife sitichidziwa?
Kodi iwe uli ndi chidziwitso chanji chimene ife tilibe?
10 Anthu a imvi ndi okalamba ali mbali yathu,
anthu amvulazakale kupambana abambo ako.
11 Kodi mawu otonthoza mtima ochokera kwa Mulungu sakukukwanira,
mawu oyankhula mofatsawa kwa iwe?
12 Chifukwa chiyani ukupsa mtima,
ndipo chifukwa chiyani ukutuzula maso ako,
13 moti ukupsera mtima Mulungu
ndi kuyankhula mawu otero pakamwa pako?
14 “Kodi munthu nʼchiyani kuti nʼkukhala woyera mtima
kapena wobadwa mwa amayi nʼchiyani kuti nʼkukhala wolungama mtima?
15 Ngati Mulungu sakhulupirira ngakhale angelo ake,
ngakhale zakumwamba sizoyera pamaso pake,
16 nanga kuli bwanji munthu amene ndi wonyansa ndi wa njira zokhotakhota,
amene kuchita zoyipa kuli ngati kumwa madzi.
17 “Mvetsera kwa ine ndipo ndidzakufotokozera;
ndilole ndikuwuze zimene ndaziona,
18 zimene anandiphunzitsa anthu anzeru,
sanandibisire kalikonse kamene anamva kuchokera kwa makolo awo.
19 (Ndi kwa iwowa kumene dziko lino linaperekedwa
pamene panalibe mlendo wokhala pakati pawo).
20 Munthu woyipa amavutika ndi masautso masiku onse a moyo wake,
munthu wankhanza adzavutika zaka zake zonse.
21 Amamva mawu owopsa mʼmakutu mwake,
pamene zonse zikuoneka ngati zili bwino, anthu achifwamba amamuthira nkhondo.
22 Iye sakhulupirira kuti angathe kupulumuka ku mdima wa imfa;
iyeyo ndi woyenera kuphedwa.
23 Amangoyendayenda pali ponse kunka nafuna chakudya;
amadziwa kuti tsiku la mdima lili pafupi.
24 Masautso ndi nthumanzi zimamuchititsa mantha kwambiri;
zimamugonjetsa iye monga imachitira mfumu yokonzekera kukathira nkhondo,
25 chifukwa iye amatambasula dzanja lake kuyambana ndi Mulungu
ndipo amadzitama yekha polimbana ndi Wamphamvuzonse.
26 Amapita mwa mwano kukalimbana naye
atanyamula chishango chochindikala ndi cholimba.
27 “Ngakhale nkhope yake ndi yonenepa
ndipo mʼchiwuno mwake muli mnofu wambiri,
28 munthuyo adzakhala mʼmizinda yowonongeka
ndi mʼnyumba zosayenera kukhalamo anthu,
nyumba zimene zikugwa ndi kuwonongeka.
29 Iye sadzalemeranso ndipo chuma chake sichidzakhalitsa,
ngakhale minda yake sidzabala zipatso pa dziko lapansi.
30 Iyeyo sadzapulumuka mu mdimamo;
lawi lamoto lidzawumitsa nthambi zake,
ndipo mpweya wochokera mʼkamwa mwa Mulungu udzamusesa.
31 Asadzinyenge yekha podalira zinthu zachabechabe,
pakuti pa mapeto pake sadzaphulapo kanthu.
32 Iye adzalandira malipiro ake nthawi yake isanakwane,
ndipo nthambi zake sizidzaphukanso.
33 Iye adzakhala ngati mtengo wamphesa wopululidwa zipatso zake zisanapse,
adzakhala ngati mtengo wa olivi umene wayoyola maluwa ake.
34 Pakuti anthu osapembedza Mulungu adzakhala osabala
ndipo moto udzapsereza nyumba za onse okonda ziphuphu.
35 Iwo amalingalira zaupandu ndipo amachita zoyipa;
mtima wawo umakonzekera zachinyengo.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.