Yesaya 29
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Tsoka kwa Mzinda wa Davide
29 Tsoka kwa iwe, Arieli, Arieli,
mzinda umene Davide anakhazikitsamo zithando za nkhondo!
Papite chaka chimodzi kapena ziwiri
ndipo masiku a zikondwerero zanu azipitirirabe ndithu.
2 Komatu Ine ndidzathira nkhondo Arieli
ndipo kudzakhala kulira ndi kudandaula,
mzindawo udzasanduka ngati ngʼanjo ya guwa lansembe.
3 Ine ndidzamanga misasa ya nkhondo kulimbana ndi mzindawo;
ndidzakuzungulira ndi nsanja za nkhondo
ndi kumanga mitumbira yanga ya nkhondo kulimbana nawe.
4 Utagwetsedwa pansi, iwe udzayankhula kuchokera mʼnthaka,
mawu ako adzatuluka uli mʼfumbi,
adzamveka ngati a mzukwa.
Mawu ako adzamveka ngati onongʼona kuchokera mʼfumbi.
5 Koma chigulu cha adani ako chidzasanduka chifwirimbwiti.
Chigulu cha ankhondo achilendo chidzabalalika ngati mungu wowuluzika ndi mphepo.
Mwadzidzidzi ndi mosayembekezereka,
6 Yehova Wamphamvuzonse adzabwera
ndi mabingu ndi chivomerezi ndi phokoso lalikulu,
kamvuluvulu ndi namondwe ndi malawi a moto wonyeketsa.
7 Tsono chigulu chankhondo cha mitundu ina yonse chimene chikulimbana ndi mzinda wa Arieli
nʼkumathira nkhondo mzindawo, malinga ake ndi kuwuzinga,
chigulu chonsecho chidzazimirira ngati maloto,
gati zinthu zoziona mʼmasomphenya usiku.
8 Chidzakhala ngati munthu wanjala wolota akudya,
koma podzuka ali nayobe njala;
kapena ngati munthu waludzu wolota akumwa,
koma podzuka, ali nalobe ludzu, kummero kwake kuli gwaa.
Izi zidzachitika pamene chigulu cha nkhondo cha mitundu ina yonse
chikunthira nkhondo Phiri la Ziyoni.
9 Pitirizani kuledzera ndipo mudzakhala opusa.
Dzitsekeni mʼmaso ndipo mukhale osapenya,
ledzerani, koma osati ndi vinyo,
dzandirani, koma osati ndi mowa.
10 Yehova wakugonetsani tulo tofa nato.
Watseka maso anu, inu aneneri;
waphimba mitu yanu, inu alosi.
11 Kwa inu mawu onsewa ali ngati buku lotsekedwa, ndipo ngati lipatsidwa kwa wina wodziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde tawerengani bukuli,” iye adzati, “Sindingathe popeza ndi lomatidwa.” 12 Kapena ngati lipatsidwa kwa amene sadziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde werenga bukuli,” iye adzayankha kuti, “Ine sindidziwa kuwerenga.”
13 Ambuye akuti,
“Anthu awa amandipembedza Ine ndi pakamwa pawo,
ndi kundilemekeza Ine ndi milomo yawo,
koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.
Kundipembedza kwawo ndi kwa chiphamaso.
Amandipembedza motsata malamulo a anthu amene anaphunzitsidwa.
14 Nʼchifukwa chakenso Ine ndidzapitirira
kuwachitira ntchito zodabwitsa;
nzeru za anthu anzeru zidzatha,
luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”
15 Tsoka kwa amene amayesetsa
kubisira Yehova maganizo awo,
amene amachita ntchito zawo mu mdima nʼkumanena kuti,
“Ndani amene akundiona kapena ndani akudziwa zimene ndikuchita?”
16 Inu mumazondotsa zinthu
ngati kuti dothi lasanduka wowumba mbiya.
Kodi chinthu chopangidwa chingawuze wochipanga kuti
“Sunandipange ndi iwe?”
Kapena mʼphika kunena kwa amene anawuwumba kuti,
“Iwe sudziwa chilichonse?”
17 Kodi Lebanoni posachedwapa sadzasanduka munda wachonde,
ndipo kodi munda wachondewo ngati nkhalango?
18 Tsiku limenelo anthu osamva adzamva mawu a mʼbuku,
ndipo anthu osaona amene
ankakhala mu mdima adzapenya.
19 Anthu odzichepetsa adzakhalanso ndi chimwemwe mwa Yehova;
ndipo anthu osowa adzakondwa chifukwa cha Woyerayo wa Israeli.
20 Koma anthu ankhanza adzazimirira,
oseka anzawo sadzaonekanso,
ndipo onse okopeka ndi zoyipa adzawonongedwa.
21 Yehova adzalanga amene amasinjirira munthu kuti apezeke wolakwa,
kapena kuphophonyetsa anthu ozenga mlandu
ndi umboni wonama kuti osalakwa asaweruzidwe mwachilungamo.
22 Choncho Yehova amene anawombola Abrahamu, akunena kwa zidzukulu za Yakobo kuti,
“Anthu anga sadzachitanso manyazi;
nkhope zawo sizidzagwanso ndi manyazi.
23 Akadzaona ana awo ndi
ntchito ya manja anga pakati pawo,
adzatamanda dzina langa loyera;
adzazindikira kuyera kwa Woyerayo wa Yakobo,
ndipo adzachita naye mantha Mulungu wa Israeli.
24 Anthu opusa adzapeza nzeru;
onyinyirika adzalandira malangizo.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.