Yesaya 24
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Chilango cha Yehova pa Dziko Lapansi
24 Taonani, Yehova adzawononga dziko lapansi
ndi kulisandutsa chipululu;
Iye adzasakaza maonekedwe ake
ndi kumwaza anthu ake onse.
2 Aliyense zidzamuchitikira mofanana:
wansembe chimodzimodzi munthu wamba,
antchito aamuna mofanananso ndi ambuye awo aamuna,
antchito aakazi chimodzimodzi ambuye awo aakazi,
wogula chimodzimodzi wogulitsa,
wobwereka chimodzimodzi wobwereketsa,
okongola chimodzimodzi okongoza.
3 Dziko lapansi lidzawonongedwa kwathunthu
ndi kusakazikiratu.
Yehova wanena mawu awa.
4 Dziko lapansi likulira ndipo likufota,
dziko lonse likuvutika ndipo likuwuma,
anthu omveka a dziko lapansi akuvutika.
5 Anthu ayipitsa dziko lapansi;
posamvera malangizo ake;
pophwanya mawu ake
ndi pangano lake lamuyaya.
6 Nʼchifukwa chake matemberero akuwononga dziko lapansi;
anthu a mʼdzikomo akuzunzika chifukwa cha kulakwa kwawo,
iwo asakazika
ndipo atsala ochepa okha.
7 Vinyo watsopano watha ndipo mphesa zikufota;
onse okonda zosangalatsa ali ndi chisoni.
8 Kulira kokometsera kwa matambolini kwatha,
phokoso la anthu osangalala latha,
zeze wosangalatsa wati zii.
9 Anthu sadzayimbanso akumwa vinyo;
akadzamwa zaukali zidzakhala zowawa mʼkamwa mwawo.
10 Mzinda wachisokonezo uja wawonongeka;
nyumba iliyonse yatsekedwa.
11 Anthu akulira mʼmisewu kufuna vinyo;
chimwemwe chonse chatheratu,
palibenso chisangalalo pa dziko lapansi.
12 Mzinda wasanduka bwinja
zipata zake zagumuka.
13 Zimenezi ndizo zidzachitikire mitundu yonse ya dziko lapansi
ndiponso pakati pa mitundu ya anthu.
Zidzakhala ngati pamene mitengo ya olivi yayoyoledwa,
kapena ngati nthawi ya kunkha la mphesa atatsiriza kukolola.
14 Koma otsala onse akufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe;
anthu akumadzulo akutamanda ukulu wa Yehova.
15 Nʼchifukwa chake inu akummawa, tamandani Yehova;
ndi inu okhala mʼmphepete mwa nyanja kwezani dzina la Yehova, Mulungu wa Israeli.
16 Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi tikumva kuyimba kotamanda
“Wolungamayo.”
Koma ine ndinati, “Ndatheratu, ndatheratu!
Tsoka kwa ine!
Anthu achinyengo akupitirizabe kuchita zachinyengo,
inde chinyengo chawo chikunkerankera mʼtsogolo.”
17 Inu anthu adziko lapansi, zoopsa, dzenje
ndi msampha zikukudikirani.
18 Aliyense wothawa phokoso la zoopsa
adzagwa mʼdzenje;
ndipo aliyense wotuluka mʼdzenjemo
adzakodwa ndi msampha.
Zitseko zakumwamba zatsekulidwa,
ndipo maziko a dziko lapansi agwedezeka.
19 Dziko lapansi lathyokathyoka,
ndipo lagawika pakati,
dziko lapansi lagwedezeka kotheratu.
20 Dziko lapansi likudzandira ngati munthu woledzera
likugwedezeka ndi mphepo ngati chisimba;
lalemedwa ndi machimo ake.
Lidzagwa ndipo silidzadzukanso.
21 Tsiku limenelo Yehova adzalanga
amphamvu a kumwamba
ndiponso mafumu apansi pano.
22 Mulungu adzawasonkhanitsa pamodzi
ngati amʼndende amene ali mʼdzenje.
Adzawatsekera mʼndende
ndipo adzalangidwa patapita nthawi yayitali.
23 Mwezi udzanyazitsidwa, dzuwa lidzachita manyazi;
pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzakhala mfumu ndipo adzalamulira;
pa Phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu,
ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.