Yeremiya 13
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Lamba Womanga Mʼchiwuno
13 Yehova anandiwuza kuti, “Pita kagule lamba wansalu yosalala ndipo ukavale mʼchiwuno mwako, koma usakamuviyike mʼmadzi.” 2 Choncho ndinakagula lambayo, monga momwe anandiwuzira Yehova, ndipo ndinamanga mʼchiwuno mwanga.
3 Kenaka Yehova anandiyankhulanso kachiwiri kuti, 4 “Tenga lamba amene unagula ndi kuvala mʼchiwuno mwako uja. Tsono pita ku mtsinje wa Yufurate ndipo ukamubise lambayo mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.” 5 Ndipo ndinapitadi ndi kukabisa lambayo ku Yufurate, monga anenera Yehova.
6 Patapita masiku ambiri Yehova anandiwuzanso kuti, “Pitanso ku Yufurate ndipo ukatenge lamba amene ndinakuwuza kuti ukamubise kumeneko.” 7 Choncho ndinapita ku Yufurate kukafukula lambayo ndi kumuchotsa pamalo pamene ndinamubisa, koma nthawi imeneyi nʼkuti lambayo atawonongeka kotheratu ndipo analibenso ntchito.
8 Pamenepo Yehova anandiwuza kuti, 9 “Izi ndi zimene ine ndikunena: ‘Umu ndi mmene ndidzawonongere zimene akunyadira kwambiri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. 10 Anthuwa ndi oyipa. Iwo akana kumvera mawu anga. Mʼmalo mwake amawumirira kutsata milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Anthu amenewa adzakhala ngati lamba wopanda ntchitoyu. 11 Monga momwe lamba amakanirira mʼchiwuno cha munthu, momwemonso ndinakonza kuti nyumba yonse ya Israeli ndi nyumba yonse ya Yuda indikangamire Ine kuti akhale anthu anga, kuti azitamanda dzina langa ndi kulemekeza Ine. Koma iwo sanamvere,’ akutero Yehova.
Zikopa Zothiramo Vinyo
12 “Awuze anthuwo kuti, ‘Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Mtsuko uliwonse adzawudzaza ndi vinyo.’ Ndipo ngati iwo anena kwa iwe kuti, ‘Kodi ngati ife sitikudziwa kuti mtsuko uliwonse udzadzazidwa ndi vinyo?’ 13 Tsono iwe uwawuze kuti, Yehova akuti ‘Ine ndidzaledzeretsa anthu onse okhala mʼdziko muno, kuyambira mafumu amene amakhala pa mpando waufumu wa Davide, ansembe, aneneri, pamodzi ndi anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu. 14 Ndidzawagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha ngati mitsuko, makolo ndi ana awo, akutero Yehova. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo kapena kukhudzidwa nawo kuti ndileke kuwawononga.’ ”
Yuda Adzapita ku Ukapolo
15 Imvani inu Aisraeli ndipo tcherani khutu,
musadzitukumule,
pakuti ndi Yehova amene akuyankhula.
16 Lemekezani Yehova Mulungu wanu
asanagwetse mdima,
mapazi anu asanayambe kupunthwa
mʼchisisira chamʼmapiri.
Asanasandutse kuwala
mukuyembekezerako kukhala
mdima wandiweyani.
17 Koma ngati simumvera,
ndidzalira kwambiri
chifukwa cha kunyada kwanu.
Mʼmaso mwanga
mwadzaza ndi misozi yowawa
chifukwa nkhosa za Yehova zatengedwa ukapolo.
18 Uza mfumu pamodzi ndi amayi ake kuti,
“Tsikani pa mipando yaufumuyo,
pakuti zipewa zanu zaufumu zokongolazo
zagwa pansi.”
19 Mizinda ya ku Negevi yatsekedwa
ndipo palibe wina woti nʼkuyitsekula.
Yuda yense watengedwa kupita ku ukapolo,
watengedwa yense ukapolo.
20 Tukula maso ako kuti uwone
amene akubwera kuchokera kumpoto.
Kodi nkhosa zimene anakusungitsa zili kuti,
nkhosa zanu zokongola zija?
21 Kodi udzanena chiyani pamene [Yehova] adzakuyikira
anthu amene unkanena kuti ndi abale ako akukugonjetsa ndi kukulamulira?
Kodi sudzamva zowawa
ngati za mayi pa nthawi yake yochira?
22 Ndipo ngati udzadzifunsa kuti,
“Kodi zimenezi zandichitikira chifukwa chiyani?”
Ndi chifukwa cha machimo anu ambiri
kuti zovala zanu zingʼambike
ndiponso kuti akuchitireni nkhanza.
23 Kodi wa dziko la Kusi nʼkusintha khungu lake,
kapena kambuku kusintha mawanga ake?
Inunso amene munazolowera kuchita
zoyipa simungathe kusintha.
24 “Ine ndidzakumwazani ngati mankhusu
amene amawuluka ndi mphepo ya ku chipululu.
25 Limeneli ndiye gawo lanu,
chilango chimene ndakukonzerani
chifukwa chondiyiwala Ine
ndi kutumikira milungu yabodza,
akutero Yehova.
26 Ine ndidzakwinya zovala zanu mpaka ku maso
kuti umaliseche wanu uwonekere.
27 Ndaona zonyansa zanu: zigololo zanu, kutchetcherera kwanu
ndi ziwerewere zanu,
zochitika pa mapiri ndi mʼminda.
Tsoka iwe Yerusalemu!
Udzakhala wosayeretsedwa
pa zachipembedzo mpaka liti?”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.