Nyimbo ya Solomoni 4
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwamuna
4 Ndiwe wokongoladi wokondedwa wanga!
Ndithudi, ndiwe wokongola!
Maso ako ali ngati nkhunda kumbuyo kwa nsalu yophimba kumutu.
Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi
zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi.
2 Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zomwe zangometedwa kumene,
zochokera kozisambitsa kumene.
Iliyonse ili ndi ana amapasa;
palibe imene ili yokha.
3 Milomo yako ili ngati mbota yofiira;
pakamwa pako ndi pokongola kwambiri.
Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yophimba
kumutuyo, masaya ako akuoneka ngati mabandu a makangadza.
4 Khosi lako lili ngati nsanja ya Davide,
yomangidwa bwino ndi yosalala;
pa nsanja imeneyo pali zishango 1,000,
zishango zonsezo za anthu ankhondo.
5 Mawere ako ali ngati tiana tiwiri ta nswala,
ngati ana amapasa a nswala
amene akudya pakati pa maluwa okongola.
6 Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira
ndipo mithunzi ikayamba kuthawa,
ndidzapita ku phiri la mure
ndi ku chitunda cha lubani.
7 Ndiwe wokongola kwambiri wokondedwa wanga;
palibe chilema pa iwe.
8 Tiye tichoke ku Lebanoni iwe mkwatibwi wanga,
tiye tichoke ku Lebanoni,
utsikepo pa msonga ya Amana,
kuchoka pa msonga ya phiri la Seniri, pamwamba penipeni pa Herimoni,
kuchoka ku mapanga a mikango
ndiponso kumapiri kumene akambuku amavutitsa.
9 Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, wanditenga mtima,
iwe wanditenga mtima
ndi kapenyedwe ka maso ako,
ndiponso ndi umodzi mwa mikanda ya mʼkhosi mwako.
10 Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, chikondi chako nʼchosangalatsa!
Chikondi chako nʼchosangalatsa kwambiri kupambana vinyo,
ndiponso fungo la mafuta ako ndi lopambana zonunkhiritsa zonse!
11 Iwe mkwatibwi wanga, milomo yako ikuchucha uchi ngati chisa cha njuchi;
pansi pa lilime lako pali mkaka ndi uchi.
Fungo lonunkhira la zovala zako likumveka ngati fungo la ku Lebanoni.
12 Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, ndiwe munda wopiringidzidwa;
ndiwe kasupe wotchingidwa, chitsime chotetezedwa.
13 Zomera zako ndi munda wa zipatso za makangadza;
muli zipatso zokoma kwambiri,
muli hena ndi nadi,
14 nadi ndi safiro,
kalamusi ndi sinamoni,
komanso mtengo uliwonse wonunkhira bwino.
Mulinso mure ndi aloe
ndi zonunkhiritsa zonse zabwino kwambiri.
15 Iwe ndiwe kasupe wa mʼmunda,
chitsime cha madzi oyenda,
mtsinje wa madzi ochokera ku Lebanoni.
Mkazi
16 Dzuka, iwe mphepo yakumpoto,
ndipo bwera, iwe mphepo yakummwera!
Uzira pa munda wanga,
kuti fungo lake lonunkhira lifalikire ponseponse.
Bwenzi langa alowe mʼmunda mwake
ndi kudya zipatso zake zabwino kwambiri.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.