Numeri 29
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Chikondwerero cha Malipenga
29 “ ‘Pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. Ili ndi tsiku limene muziliza malipenga. 2 Muzipereka mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi wopanda chilema monga nsembe zopsereza, fungo lokoma kwa Yehova. 3 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse, muzipereka chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Pa nkhosa yayimuna iliyonse muzipereka makilogalamu awiri. 4 Pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiri aja muzipereka kilogalamu imodzi. 5 Muziperekanso mbuzi yayimuna kuti izikhala nsembe yopepesera machimo anu. 6 Izi ndi zowonjezera pa nsembe zopsereza za mwezi ndi mwezi komanso za tsiku ndi tsiku pamodzi ndi zopereka za chakudya ndi zopereka za chakumwa potsata malamulo ake. Izi ndi zopereka zotentha pa moto, zoperekedwa kwa Yehova, fungo lokoma.
Tsiku la Mwambo Wopepesera Machimo
7 “ ‘Pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiwiriwu, muzichita msonkhano wopatulika. Muzisala zakudya ndipo musamagwire ntchito. 8 Muzipereka kwa Yehova nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokoma lokondweretsa Yehovayo; ngʼombe yayimuna imodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi. Zimenezi zizikhala zopanda chilema. 9 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; pa nkhosa yayimuna iliyonse makilogalamu awiri; 10 kilogalamu imodzi pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiriwo. 11 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna kuti izikhala nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe yopepesera machimo ya pa tsiku la mwambo ija, kuwonjezanso pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi cha chakumwa.
Chikondwerero cha Misasa
12 “ ‘Pa tsiku la mwezi wachisanu ndi chiwiri, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. Muzichita madyerero a Yehova masiku asanu ndi awiri. 13 Muzipereka nsembe yotentha pa moto, kuti izikhala fungo lokoma kwa Yehova, nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna khumi ndi atatu, nkhosa zazimuna ziwiri, ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema. 14 Pa mwana wangʼombe aliyense mwa ana angʼombe aamuna khumi ndi atatu aja, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Pa nkhosa iliyonse mwa nkhosa ziwiri zija, mukonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu awiri. 15 Pa mwana wankhosa aliyense mwa ana ankhosa aamuna khumi ndi anayiwo, muzipereka chakudya cha kilogalamu imodzi. 16 Muziperekanso mbuzi yayimuna imodzi kuti izikhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
17 “ ‘Pa tsiku lachiwiri muzipereka ana angʼombe aamuna khumi ndi awiri aja, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi aja, zonse zopanda chilema. 18 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka zopereka za chakudya ndi za chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. 19 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
20 “ ‘Pa tsiku lachitatu muzipereka ngʼombe zazimuna khumi ndi imodzi, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema. 21 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka zopereka za chakudya ndi za chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. 22 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
23 “ ‘Pa tsiku lachinayi muzipereka ngʼombe zazimuna khumi, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema. 24 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. 25 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
26 “ ‘Pa tsiku lachisanu muzipereka ngʼombe zazimuna zisanu ndi zinayi, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema. 27 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. 28 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
29 “ ‘Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi muzipereka ngʼombe zazimuna zisanu ndi zitatu, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema. 30 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. 31 Muziperekenso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
32 “ ‘Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzipereka ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa amuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema. 33 Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. 34 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
35 “ ‘Pa tsiku lachisanu ndi chitatu muzichita msonkhano ndipo musamagwire ntchito iliyonse. 36 Muzipereka chopereka chotentha pa moto monga fungo lokoma kwa Yehova, nsembe yopsereza ya ngʼombe imodzi yayimuna, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa amuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema. 37 Pamodzi ndi ngʼombe yayimunayo, nkhosa yayimunayo ndi ana ankhosawo, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo. 38 Muziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, powonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.
39 “ ‘Kuwonjezera pa zopereka zimene munalumbirira ndi pa zopereka zanu zaufulu, muzipereka zimenezi kwa Yehova pa masiku osankhika a chikondwerero chanu. Nsembe zanu zachakumwa ndi nsembe zanu zachiyanjano.’ ”
40 Mose anawuza Aisraeli zonse zimene Yehova anamulamulira.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.