Miyambo 6
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Za Moyo wa Uchitsiru
6 Mwana wanga, ngati wamuperekera mnansi wako chikole,
ngati walonjeza kumulipirira mlendo,
2 ngati wagwidwa ndi zimene iwe unanena,
wakodwa ndi mawu a mʼkamwa mwako.
3 Tsono popeza iwe mwana wanga
wadziponya mʼmanja mwa mnansi wako, chita izi kuti udzipulumutse:
pita msanga ukamupemphe mnansi wako;
kuti akumasule!
4 Usagone tulo,
usawodzere.
5 Dzipulumutse monga imachitira mphoyo mʼdzanja la mlenje,
ndi monga imachitira mbalame mu msampha wa munthu wosaka.
6 Pita kwa nyerere, mlesi iwe;
kaonetsetse njira zake kuti uphunzirepo kanthu!
7 Zilibe mfumu,
zilibe woyangʼanira kapena wolamulira,
8 komabe zimasungiratu chakudya chake nthawi ya chilimwe
ndipo zimatuta chakudyacho nthawi yokolola.
9 Kodi uzingogonabe pamenepo mpaka liti mlesi iwe?
Kodi tulo tako tidzatha liti?
10 Ukati ndingogona pangʼono, ndingowodzera pangʼono
ndingopinda manjawa pangʼono kuti ndipumule,
11 umphawi udzakugwira ngati mbala
ndipo usiwa udzafika ngati munthu wachifwamba.
12 Munthu wachabechabe, munthu woyipa,
amangoyendayenda ndi kumayankhula zoyipa,
13 amatsinzinira maso ake,
namakwakwaza mapazi ake
ndi kulozaloza ndi zala zake,
14 amalingalira zoyipa ndi mtima wake wachinyengo
ndipo nthawi zonse amangokhalira kuyambitsa mikangano pakati pa anthu.
15 Nʼchifukwa chake tsoka lidzamugwera modzidzimutsa;
adzawonongeka msangamsanga popanda chomupulumutsa.
16 Pali zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Yehova amadana nazo,
zinthu zisanu ndi ziwiri zimene zimamunyansa:
17 maso onyada,
pakamwa pabodza,
manja akupha munthu wosalakwa,
18 mtima wokonzekera kuchita zoyipa,
mapazi othamangira msanga ku zoyipa,
19 mboni yonama yoyankhula mabodza
komanso munthu amene amayambitsa mikangano pakati pa abale.
Chenjezo pa za Chigololo
20 Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako;
ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako.
21 Zimenezi uzimatirire pa mtima pako masiku onse,
uzimangirire mʼkhosi mwako.
22 Ukamayenda, zidzakulozera njira;
ukugona, zidzakulondera;
ukudzuka, zidzakuyankhula.
23 Paja malamulo awa ali ngati nyale,
malangizowa ali ngati kuwunika,
ndipo chidzudzulo cha mwambo ndiwo
moyo weniweni,
24 kukupulumutsa kwa mkazi wadama,
zimenezi zidzakutchinjiriza kwa mkazi wadama, ndi kukuthandiza kuti usamvere mawu oshashalika a mkazi wachiwerewere.
25 Mu mtima wako usakhumbire kukongola kwake,
asakukope ndi zikope zake,
26 paja mkazi wadama amakusandutsa kukhala ngati nyenyeswa za buledi
ndipo mkazi wa mwini wake amasokonezeratu moyo wako wonse.
27 Kodi munthu angathe kutenga moto
zovala zake osapsa?
28 Kodi munthu angathe kuyenda pa makala amoto
mapazi ake osapserera?
29 Ndizo zimachitikira munthu amene amagonana ndi mkazi wa munthu wina.
Aliyense wokhudza mkazi wotere adzalangidwa.
30 Paja anthu sayinyoza mbala ikaba
chifukwa chakuti ili ndi njala.
31 Komabe ngati mbalayo igwidwa iyenera kulipira kasanu nʼkawiri,
ngakhale kulandidwa katundu wa mʼnyumba mwake.
32 Munthu wochita chigololo ndi wopanda nzeru.
Wochita zimenezi amangodziwononga yekha.
33 Adzalandira mabala ndi mʼnyozo,
ndipo manyazi ake sadzamuchokera.
34 Paja nsanje imachititsa mwini mkaziyo kukalipa,
ndipo sadzachita chifundo pobwezera.
35 Iye savomera dipo lililonse;
sangapepeseke ngakhale umupatse mphatso zochuluka motani.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.