Ahebri 8
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mkulu wa Ansembe wa Pangano Latsopano
8 Fundo yayikulu pa zimene tikunenazi ndi iyi: Tili naye ife Mkulu wa ansembe, amene anakhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu Waulemerero kumwamba. 2 Ndipo akutumikira mʼmalo opatulika, mu Tenti yeniyeni yoyikidwa ndi Ambuye, osati ndi munthu.
3 Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuti azipereka mphatso ndi nsembe kwa Mulungu, ndipo kunali koyenera kuti wansembe wathunso akhale nʼkanthu kopereka. 4 Ngati iye akanakhala pa dziko lapansi, sakanakhala wansembe pakuti alipo kale anthu amene amapereka mphatso zolembedwa mʼMalamulo. 5 Iwo amatumikira pamalo opatulika amene ndi chithunzi ndi chifanizo cha zimene zili kumwamba. Ichi ndi chifukwa chake Mose anachenjezedwa pamene anali pafupi kumanga Tenti: “Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.” 6 Koma Yesu analandira utumiki wopambana kuposa wawo monga Iyenso ali Nkhoswe ya pangano lopambana kuposa lakale lija, chifukwa pangano latsopano lakhazikika pa malonjezano opambana kwambiri.
7 Ngati pangano loyamba lija likanakhala langwiro, sipakanafunikanso lina mʼmalo mwake. 8 Koma Mulungu anapeza zolakwika pakati pa anthu ndipo anati,
“Masiku akubwera,” akutero Yehova,
“pamene ndidzachita pangano latsopano
ndi Aisraeli
ndiponso nyumba ya Yuda.
9 Silidzakhala ngati pangano
limene ndinachita ndi makolo awo,
pamene ndinawagwira padzanja
nʼkuwatulutsa ku Igupto
chifukwa iwo sanasunge pangano langa lija
ndipo Ine sindinawasamalire,
akutero Ambuye.
10 Tsono ili ndi pangano ndidzapangane ndi nyumba ya Israeli:
Atapita masiku amenewa, akutero Ambuye,
Ine ndidzayika malamulo anga mʼmaganizo mwawo,
ndi kulemba mʼmitima mwawo.
Ine ndidzakhala Mulungu wawo,
ndipo iwo adzakhala anthu anga.
11 Sipadzafunikanso wina kuti aphunzitse mnzake,
kapena munthu kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, udziwe Ambuye
chifukwa onse adzandidziwa,
kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu.
12 Pakuti Ine ndidzawakhululukira zoyipa zawo,
ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”
13 Ponena kuti, pangano “latsopano” Mulungu wapanga pangano loyamba lija kukhala lotha ntchito, ndipo chilichonse chimene chayamba kutha ntchito ndi kukalamba, chili pafupi kuchokeratu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.