2 Mbiri 23
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
23 Mʼchaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaonetsa mphamvu zake. Iye anachita pangano ndi olamulira magulu a anthu 100: Azariya mwana wa Yerohamu, Ismaeli mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maaseya mwana wa Adaya ndi Elisafati mwana wa Zikiri. 2 Iwo anayendayenda mʼdziko la Yuda ndipo anasonkhanitsa Alevi ndi atsogoleri a mabanja a Aisraeli ochokera mʼmizinda yonse. Atabwera ku Yerusalemu, 3 msonkhano wonse unachita pangano ndi mfumu mu Nyumba ya Mulungu.
Yehoyada anawawuza kuti, “Mwana wa mfumu adzalamulira monga ananenera Yehova zokhudza ana a Davide. 4 Tsopano zimene muti muchite ndi izi: Limodzi mwa magawo atatu a ansembe ndi Alevi amene mudzakhale pa ntchito pa Sabata muzikalondera pa khomo, 5 ndi limodzi la magawo atatu likakhale ku nyumba yaufumu ndipo limodzi la magawo atatu likakhale ku chipata cha Maziko ndipo anthu ena onse akakhale mʼmabwalo a Nyumba ya Yehova. 6 Musalole aliyense kulowa mʼNyumba ya Yehova kupatula ansembe ndi Alevi amene akutumikira. Iwo atha kutero chifukwa apatulidwa koma anthu ena onse ayenera kumvera zimene Yehova walamula. 7 Alevi akhale mozungulira mfumu, munthu aliyense ali ndi chida chake mʼmanja. Aliyense amene alowe mʼNyumba ya Mulungu ayenera kuphedwa. Mukhale nayo pafupi mfumu kulikonse kumene izipita.”
8 Alevi ndi anthu onse a ku Yuda anachita monga momwe wansembe Yehoyada anawalamulira. Aliyense anatenga anthu ake amene ankagwira ntchito pa Sabata ndi amene amapita kukapuma, pakuti wansembe Yehoyada sanalole gulu lililonse kuti lipite. 9 Ndipo Yehoyada anapereka kwa atsogoleri a magulu a anthu 100 mikondo ndi zishango zazikulu ndi zazingʼono zimene zinali za Davide ndipo zinali mʼNyumba ya Mulungu. 10 Iye anayika anthu onse, aliyense ali ndi chida mʼdzanja lake mozungulira mfumu pafupi ndi guwa ndi Nyumba ya Mulungu, kuyambira mbali ya kummwera mpaka kumpoto kwa Nyumba ya Mulungu.
11 Yehoyada ndi ana ake anatulutsa mwana wa mfumu ndipo anamumveka chipewa chaufumu ndipo anamupatsa Buku la Chipangano namulonga ufumu. Yehoyada ndi ana ake anamudzoza ndipo anafuwula kuti, “Ikhale ndi moyo wautali mfumu!”
12 Ataliya atamva phokoso la anthu akuthamanga ndi kukondwerera mfumu, anapita ku Nyumba ya Yehova komwe kunali anthuko. 13 Iye anayangʼana, ndipo anaona mfumu itayima pa chipilala chake chapakhomo. Atsogoleri ndi oyimba malipenga anali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a mʼderali amakondwerera ndi kuyimba malipenga ndiponso oyimba ndi zida amatsogolera matamando. Pamenepo Ataliya anangʼamba mkanjo wake ndipo anafuwula kuti, “Kuwukira! Kuwukira!”
14 Wansembe Yehoyada anatumiza olamulira magulu a anthu 100 aja, amene amayangʼanira asilikali ndipo anawawuza kuti, “Mutulutseni ameneyu pakati pa mizere yanu ndipo muphe aliyense amene adzamutsata.” Pakuti ansembe anati, “Musamuphere mʼNyumba ya Mulungu wa Yehova,” 15 choncho anamugwira pamene amafika pa chipata cha Kavalo pa bwalo la nyumba yaufumu, ndipo anamuphera pamenepo.
16 Tsono Yehoyada anachita pangano, iye mwini ndi anthu onse ndiponso mfumu kuti adzakhala anthu a Yehova. 17 Anthu onse anapita ku kachisi wa Baala ndipo anamugwetsa. Iwo anaphwanya maguwa ndi mafano ndi kupha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwawo.
18 Kenaka Yehoyada anayika ansembe, omwe anali Alevi kukhala oyangʼanira Nyumba ya Yehova, amene Davide anawapatsa ntchito yoti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova mʼNyumba ya Mulungu, monga zinalembedwa mʼmalamulo a Mose kuti azitero akukondwera ndi kuyimba monga Davide analamulira. 19 Ndipo anayika alonda a pa khomo pa zipata za Nyumba ya Yehova kuti aliyense amene ndi odetsedwa asalowe.
20 Iye anatenga olamulira magulu a anthu 100, anthu otchuka, olamulira anthu ndi anthu onse a mʼderalo ndipo anabweretsa mfumu kuchokera ku Nyumba ya Mulungu. Iwo anapita ku nyumba yaufumu kudzera ku Chipata Chakumitu ndipo anayikira mfumu mpando wolemekezeka, 21 ndipo anthu onse a mʼderali anakondwera. Tsono mu mzinda munali bata chifukwa Ataliya anaphedwa ndi lupanga.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.