Yoweli 2
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Chilango cha Mulungu
2 Lizani lipenga mu Ziyoni.
Chenjezani pa phiri langa loyera.
Onse okhala mʼdziko anjenjemere,
pakuti tsiku la Yehova likubwera,
layandikira;
2 tsiku la mdima ndi chisoni,
tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani.
Ngati mʼbandakucha umene wakuta mapiri,
gulu lalikulu ndi la ankhondo amphamvu likubwera,
gulu limene nʼkale lomwe silinaonekepo
ngakhale kutsogolo kuno silidzaonekanso.
3 Patsogolo pawo moto ukupsereza,
kumbuyo kwawo malawi amoto akutentha zinthu.
Patsogolo pawo dziko lili ngati munda wa Edeni,
kumbuyo kwawo kuli ngati chipululu,
kulibe kanthu kotsalapo.
4 Maonekedwe awo ali ngati akavalo;
akuthamanga ngati akavalo ankhondo.
5 Akulumpha pamwamba pa mapiri
ndi phokoso ngati la magaleta,
ngati moto wothetheka wonyeketsa ziputu,
ngati gulu lalikulu la ankhondo lokonzekera nkhondo.
6 Akangowaona, anthu a mitundu ina amazunzika mu mtima;
nkhope iliyonse imagwa.
7 Amathamanga ngati ankhondo;
amakwera makoma ngati asilikali.
Onse amayenda pa mizere,
osaphonya njira yawo.
8 Iwo sakankhanakankhana,
aliyense amayenda molunjika.
Amadutsa malo otchingidwa
popanda kumwazikana.
9 Amakhamukira mu mzinda,
amathamanga mʼmbali mwa khoma.
Amakwera nyumba ndi kulowamo;
amalowera pa zenera ngati mbala.
10 Patsogolo pawo dziko limagwedezeka,
thambo limanjenjemera,
dzuwa ndi mwezi zimachita mdima,
ndipo nyenyezi zimaleka kuwala.
11 Yehova amabangula
patsogolo pawo,
gulu lake lankhondo ndi losawerengeka,
ndipo amphamvu ndi amene amamvera kulamula kwake.
Tsiku la Yehova ndi lalikulu;
ndi loopsa.
Ndani adzapirira pa tsikulo?
Ngʼambani Mtima Wanu
12 “Ngakhale tsopano,
bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse
posala zakudya ndi kukhetsa misozi,” akutero Yehova.
13 Ngʼambani mtima wanu
osati zovala zanu.
Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu,
pakuti Iye ndi wokoma mtima ndi wachifundo,
wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka,
ndipo amaleka kubweretsa mavuto.
14 Akudziwa ndani? Mwina adzasintha maganizo nʼkutimvera chisoni,
nʼkutisiyira madalitso,
a chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa
kwa Yehova Mulungu wanu.
15 Lizani lipenga mu Ziyoni,
lengezani tsiku losala zakudya,
itanitsani msonkhano wopatulika.
16 Sonkhanitsani anthu pamodzi,
muwawuze kuti adziyeretse;
sonkhanitsani akuluakulu,
sonkhanitsani ana,
sonkhanitsani ndi oyamwa omwe.
Mkwati atuluke mʼchipinda chake,
mkwatibwi atuluke mokhala mwake.
17 Ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova,
alire pakati pa guwa lansembe ndi khonde la Nyumba ya Yehova.
Azinena kuti, “Inu Yehova, achitireni chifundo anthu anu.
Musalole kuti cholowa chanu chikhale chinthu chonyozeka,
kuti anthu a mitundu ina awalamulire.
Kodi nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina amanena kuti,
‘Ali kuti Mulungu wawo?’ ”
Yankho la Yehova
18 Pamenepo Yehova adzachitira nsanje dziko lake
ndi kuchitira chisoni anthu ake.
19 Yehova adzawayankha kuti,
“Ine ndikukutumizirani tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta
ndipo mudzakhuta ndithu;
sindidzakuperekaninso kuti mukhale chitonzo
kwa anthu a mitundu ina.
20 “Ine ndidzachotsa ankhondo akumpoto kuti apite kutali ndi inu,
kuwapirikitsira ku dziko lowuma ndi lachipululu,
gulu lawo lakutsogolo ndidzalipirikitsira ku nyanja ya kummawa
ndi gulu lawo lakumbuyo, ku nyanja ya kumadzulo.
Ndipo mitembo yawo idzawola,
fungo lake lidzamveka.”
Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.
21 Iwe dziko usachite mantha;
sangalala ndipo kondwera.
Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.
22 Inu nyama zakuthengo, musachite mantha,
pakuti msipu wa ku chipululu ukuphukira.
Mitengo ikubala zipatso zake;
mitengo ya mkuyu ndi mpesa ikubereka kwambiri.
23 Inu anthu a ku Ziyoni sangalalani,
kondwerani mwa Yehova Mulungu wanu,
pakuti wakupatsani
mvula yoyambirira mwachilungamo chake.
Iye wakutumizirani mivumbi yochuluka,
mvula yoyambirira ndi mvula ya nthawi ya mphukira, monga poyamba paja.
24 Pa malo opunthira padzaza tirigu;
mʼmitsuko mudzasefukira vinyo watsopano ndi mafuta.
25 “Ine ndidzakubwezerani zonse zimene zinawonongedwa ndi dzombe,
dzombe lalikulu ndi dzombe lalingʼono,
dzombe lopanda mapiko ndi dzombe lowuluka;
gulu langa lalikulu la nkhondo limene ndinalitumiza pakati panu.
26 Mudzakhala ndi chakudya chambiri, mpaka mudzakhuta,
ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu,
amene wakuchitirani zodabwitsa;
ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.
27 Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndili mu Israeli,
kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
ndi kuti palibenso wina;
ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.
Tsiku la Yehova
28 “Ndipo patapita nthawi,
ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.
Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera,
nkhalamba zanu zidzalota maloto,
anyamata anu adzaona masomphenya.
29 Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi
ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo.
30 Ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalenga
ndi pa dziko lapansi,
ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo.
31 Dzuwa lidzadetsedwa
ndipo mwezi udzaoneka ngati magazi
lisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Ambuye.
32 Ndipo aliyense amene adzayitana
pa dzina la Ambuye adzapulumuka;
pakuti chipulumutso chidzakhala pa Phiri la Ziyoni
ndi mu Yerusalemu,
monga Yehova wanenera,
pakati pa otsala
amene Yehova wawayitana.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.