Yohane 11
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Imfa ndi Kuukitsidwa kwa Lazaro
11 Tsopano munthu wina dzina lake Lazaro anadwala. Iye anali wa ku Betaniya, mudzi wa Mariya ndi mchemwali wake Marita. 2 Mariyayo ndi yemwe uja amene anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake. Lazaro wodwalayo anali mlongo wake. 3 Choncho alongo ake anatumiza mawu kwa Yesu kuti, “Ambuye, uja amene Inu mumamukonda akudwala.”
4 Atamva izi, Yesu anati, “Kudwalako safa nako. Koma akudwala kuti Mulungu alemekezedwe; ndi kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe chifukwa cha matendawo.” 5 Yesu anakonda Marita, mchemwali wake ndi Lazaro. 6 Koma atamva kuti Lazaro akudwala, Iye anakhalabe kumene anali masiku ena awiri.
7 Kenaka anati kwa ophunzira ake, “Tiyeni tibwerere ku Yudeya.”
8 Ophunzira akewo anati, “Rabi, posachedwa pomwepa Ayuda anafuna kukugendani ndi miyala, koma Inu mukupitanso komweko?”
9 Yesu anayankha kuti, “Kodi sipali maora khumi ndi awiri pa tsiku? Munthu amene amayenda masana sapunthwa, popeza akuona chifukwa cha kuwala kwa dziko lapansi. 10 Koma amene akuyenda usiku amapunthwa, chifukwa kuwalako alibe.”
11 Iye atatha kunena izi, anapitirira kuwawuza iwo kuti, “Bwenzi lathu Lazaro wagona tulo; koma Ine ndikupita kumeneko kukamudzutsa.”
12 Ophunzira ake anayankha kuti, “Ambuye, ngati wagona adzapeza bwino.” 13 Yesu ankayankhula za imfa yake koma ophunzira ake ankaganiza kuti amanena za tulo chabe.
14 Ndipo kenaka anawawuza momveka kuti, “Lazaro wamwalira. 15 Ine ndikukondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe kumeneko; koma kuti mukakhulupirire tiyeni tipiteko.”
16 Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira anzake, “Tiyeni nafenso tipite, kuti tikafere naye pamodzi.”
Yesu Atonthoza Alongo a Lazaro
17 Yesu atafika, anapeza kuti Lazaro anali atagona mʼmanda masiku anayi. 18 Mudzi wa Betaniya unali pafupi ndi Yerusalemu pa mtunda wosachepera makilomita atatu, 19 ndipo Ayuda ambiri anabwera kwa Marita ndi Mariya kudzawatonthoza pa imfa ya mʼbale wawo. 20 Pamene Marita anamva kuti Yesu akubwera, anapita kukakumana naye. Koma Mariya anatsala ku nyumba.
21 Marita anati kwa Yesu, “Ambuye, mukanakhala muli kuno, mlongo wanga sakanamwalira. 22 Koma ine ndikudziwa kuti ngakhale tsopano Mulungu adzakupatsani chilichonse chimene mudzamupempha.”
23 Yesu anati kwa iye, “Mlongo wako adzauka.”
24 Marita anayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti adzauka pa kuukanso pa tsiku lomaliza.”
25 Yesu anati kwa iye, “Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo. 26 Aliyense amene ali ndi moyo ndi kukhulupirira Ine sadzamwalira. Kodi iwe ukukhulupirira izi?”
27 Marita anamuwuza Iye kuti, “Inde Ambuye, ine ndikukhulupirira kuti ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene abwera mʼdziko lapansi.”
28 Ndipo iye atanena izi anabwerera ndi kukayitana mchemwali wake Mariya namuyankhula monongʼona pambali, nati, “Aphunzitsi abwera ndipo akukuyitana.” 29 Mariya atamva izi, anayimirira mofulumira napita kwa Iye. 30 Tsopano nʼkuti Yesu asanalowe mʼmudzi, koma anali akanali pa malo pamene Marita anakumana naye. 31 Ayuda amene ankamutonthoza Mariya mʼnyumba, anaona mmene iye anayimira mofulumira ndi kutuluka kunja, iwo anamutsata akuganizira kuti ankapita ku manda kukalirira kumeneko.
32 Mariya anafika pamalo pamene panali Yesu ndipo atamuona, anagwa pa mapazi ake ndipo anati, “Ambuye mukanakhala muli kuno mlongo wanga sakanamwalira.”
33 Yesu ataona iye akulira, ndi Ayuda amene anabwera naye akuliranso, anakhudzidwa kwambiri ndi kuvutika mu mzimu. 34 Iye anafunsa kuti, “Kodi mwamuyika kuti?”
Iwo anayankha kuti, “Ambuye tiyeni mukaone.”
35 Yesu analira.
36 Pamenepo Ayuda anati, “Taonani mmene Iye anamukondera Lazaro!”
37 Koma ena a iwo anati, “Iye amatsekula maso a munthu wosaona, kodi sakanakhoza kuletsa kuti munthu uyu asamwalire?”
Yesu Aukitsa Lazaro
38 Yesu atakhudzidwanso kwambiri anafika ku manda. Manda akewo anali phanga ndipo anatsekapo ndi mwala. 39 Yesu anati, “Chotsani mwala.”
Marita mlongo wa womwalirayo anati, “Koma Ambuye, nthawi ino wayamba kununkha, pakuti wakhala mʼmenemu masiku anayi.”
40 Kenaka Yesu anati, “Kodi Ine sindinakuwuze kuti ngati iwe ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?”
41 Choncho iwo anachotsa mwalawo. Kenaka Yesu anayangʼana kumwamba ndikuti, “Atate, Ine ndikukuthokozani chifukwa mumandimvera. 42 Ine ndimadziwa kuti Inu mumandimvera nthawi zonse, koma Ine ndanena izi chifukwa cha anthu amene ayima pano, kuti iwo akhulupirire kuti Inu munandituma Ine.”
43 Yesu atanena izi, Iye anayitana ndi mawu ofuwula kuti, “Lazaro, tuluka!” 44 Munthu womwalirayo anatuluka, womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za ku manda, ndi nkhope yake yokulungidwa nsalu.
Yesu anawawuza kuti, “Mʼmasuleni, ndipo muloleni apite.”
Ayuda Apangana za Kupha Yesu
45 Choncho Ayuda ambiri amene anabwera kudzamuchereza Mariya ndi kuona zimene Yesu anachita anamukhulupirira Iye. 46 Koma ena a iwo anapita kwa Afarisi ndi kukawawuza zimene Yesu anachita. 47 Kenaka akulu a ansembe ndi Afarisi anayitanitsa msonkhano wa akulu olamulira.
Iwo anafunsa kuti, “Kodi ife tikuchita chiyani? Pano pali munthu uyu akuchita zizindikiro zodabwitsa zambiri. 48 Ngati ife timuleka kuti apitirize chotere, aliyense adzamukhulupirira Iye, ndipo kenaka Aroma adzabwera ndi kudzatenga malo athu pamodzi ndi dziko lathu.”
49 Kenaka mmodzi wa iwo, dzina lake Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho, anayankhula kuti, “Inu simukudziwa kanthu kalikonse! 50 Inu simukuzindikira kuti kuli bwino kwa inu kuti munthu mmodzi afe mʼmalo mwa anthu kusiyana ndi kuti mtundu wonse uwonongeke.”
51 Iye sananene izi mwa iye yekha, koma monga mkulu wa ansembe chaka chimenecho ananenera kuti Yesu anayanera kufera mtundu wa Ayuda, 52 ndipo osati mtundu okhawo komanso kwa ana ena a Mulungu onse obalalikana, kuti awabweretse pamodzi ndi kuwapanga kukhala amodzi. 53 Choncho kuyambira tsiku limeneli iwo anakonzekera za kuti amuphe.
54 Chifukwa cha ichi Yesu sanayendenso moonekera pakati pa Ayuda. Mʼmalo mwake Iye anapita ku chigawo cha kufupi ndi chipululu, ku mudzi wa Efereimu, kumene Iye anakhalako ndi ophunzira ake.
55 Nthawi ya Paska wa Ayuda itayandikira, ambiri anakwera kupita ku Yerusalemu kuchokera ku madera a ku midzi chifukwa cha mwambo wa kuyeretsedwa Paska asanafike. 56 Iwo anapitiriza kumufunafuna Yesu, ndipo pamene ankayimirira mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi ukuganiza chiyani? Kodi Iye sabwera konse kuphwando?” 57 Koma akulu a ansembe ndi Afarisi anapereka lamulo kuti ngati wina aliyense adziwe kumene kunali Yesu, iye akawawuze kuti akamugwire.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.