Yobu 41
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
41 “Kodi ungathe kukoka ngʼona ndi mbedza ya nsomba
kapena kukanikiza lilime lake pansi ndi chingwe?
2 Kodi ungathe kumanga chingwe mʼmphuno mwake,
kapena kubowola nsagwada zake ndi mbedza?
3 Kodi ngʼonayo idzakupempha kuti uyichitire chifundo?
Kodi idzakuyankhula ndi mawu ofatsa?
4 Kodi idzachita nawe mgwirizano
kuti uyisandutse kapolo wako mpaka muyaya?
5 Kodi udzasewera nayo ngati mbalame,
kapena kuyimangirira kuti atsikana ako asewere nayo?
6 Kodi anthu adzayitsatsa malonda?
Nanga amalondawo nʼkugawanagawana nyama yake kuti akagulitse?
7 Kodi chikopa chake ungathe kuchilasa ndi zisonga,
kapena kubowola mutu wake ndi nthungo zophera nsomba?
8 Ukayiputa udziwe kuti pali nkhondo,
ndipo iweyo sudzabwereranso.
9 Chiyembekezo choti nʼkuyigonjetsa ndi chabodza;
kungoyiona kokha, ndithu iwe kumangodzigwera wekha.
10 Palibe wolimba mtima kuti ndi kuyiputa.
Ndani angalimbe mtima kulimbana ndi Ine?
11 Kodi ndani anandipatsa kanthu kuti ndimubwezere?
Zonse za pansi pa thambo ndi zanga.
12 “Sindidzaleka kuyankhula za ziwalo zake za chirombocho,
za mphamvu zake ndiponso za maonekedwe a thupi lake.
13 Ndani angasende chikopa chake?
Ndani angayiyandikire kuti abowole chikopa chake cholimbacho?
14 Ndani angatsekule kukamwa kwake,
pakamwa pamene pazunguliridwa ndi mano ochititsa mantha?
15 Kumsana kwake kuli mizere ya mamba
onga zishango zolumikizanalumikizana;
16 Mambawo ndi olukanalukana
kotero kuti mpweya sungathe kulowa pakati pake.
17 Ndi olumikizanalumikizana;
ndi omatirirana kwambiri kotero kuti sangathe kulekana.
18 Kuyetsemula kwake kumatulutsa mbaliwali;
maso ake amawala ngati kuwala kwa mʼbandakucha.
19 Mʼkamwa mwake mumatuluka nsakali zamoto ndipo
mumathetheka mbaliwali zamoto.
20 Mʼmphuno mwake mumatuluka utsi
ngati wa mʼnkhali yowira yomwe ili pa moto wa bango.
21 Mpweya wake umayatsa makala,
ndipo malawi amoto amatuluka mʼkamwa mwake.
22 Mphamvu zake zili mʼkhosi mwake;
aliyense wokumana nayo amangoti njenjenje ndi mantha.
23 Minyewa ya thupi lake ndi yolumikizana ndipo
ndi yokhwima kwambiri ndi yolimba.
24 Pachifuwa pake ndi powuma ngati mwala,
ndi pa gwaa, ngati mwala wamphero.
25 Ngʼonayo ikangovuwuka,
ndi anthu amphamvu omwe amaopa; amabwerera mʼmbuyo, kuthawa.
26 Ngakhale ikanthidwe ndi lupanga, lupangalo silichita kanthu,
ngakhale mkondo, muvi ndi nthungo, zonse zimalephera.
27 Chitsulo imachiyesa ngati phesi chabe
ndi mkuwa ngati chikuni chowola.
28 Muvi sungathe kuyithawitsa,
miyala imene ayilasa nayo imangoyinyenyanyenya.
29 Zibonga zimakhala ngati ziputu;
imangoseka pamene akuyibaya ndi nthungo.
30 Mamba a ku mimba kwake ali ngati chopunthira chakunthwa ndipo
imasiya mkukuluzi mʼmatope ngati galeta lopunthira tirigu.
31 Imagadutsa madzi ozama ngati madzi a mʼnkhali,
imachititsa nyanja kuti iwire ngati mbiya yoyengera mafuta.
32 Kumbuyo kwake imasiya nthubwitubwi zambee,
kotero kuti munthu angaganize kuti nyanja yachita imvi.
33 Pa dziko lapansi palibe china chofanana nacho,
nʼcholengedwa chopanda mantha.
34 Chimanyoza nyama zina zonse;
icho chija ndi mfumu ya nyama zonse.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.