Yobu 38
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Yehova Ayankhula
38 Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati:
2 “Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wanga
poyankhula mawu opanda nzeru?
3 Onetsa chamuna;
ndikufunsa
ndipo undiyankhe.
4 “Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi?
Ndiwuze ngati ukudziwa.
5 Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa!
Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli?
6 Kodi maziko ake anawakumba potani,
kapena ndani anayika mwala wake wapangodya,
7 pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi
ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa?
8 “Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa,
pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko,
9 pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chake
ndi kuyikulunga mu mdima wandiweyani,
10 pamene ndinayilembera malire ake
ndikuyikira zitseko ndi mipiringidzo yake.
11 Pamene ndinati, ‘Ufike mpaka apa ndipo usapitirire
apa ndiye pamene mafunde ako amphamvuwo azilekezera?’
12 “Kodi chibadwire chako unalamulapo dzuwa kuti lituluke mmawa,
kapena kuti mʼbandakucha ukhalepo pa nthawi yake,
13 kuti kuwalako kuwunikire dziko lonse lapansi
ndi kuthamangitsa anthu oyipa?
14 Chifukwa cha kuwala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati zilembo za chidindo pa mtapo;
zimaonekera bwino ngati makwinya a chovala.
15 Kuwala kwa dzuwako sikuwafikira anthu oyipa,
ndipo dzanja lawo silingathe kuchita kanthu.
16 “Kodi unayendapo pansi penipeni pa nyanja
kapena pa magwero ake ozama?
17 Kodi anakuonetsapo zipata za imfa?
Kodi unaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wandiweyani?
18 Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziwa?
Undiwuze ngati ukuzidziwa zonsezi.
19 “Kodi njira yopita kumene kumakhala kuwala ili kuti?
Nanga mdima umakhala kuti?
20 Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwawoko zimenezi?
Kodi ukuyidziwa njira yopita kwawoko?
21 Ndithu, iwe ukuyidziwa, poti paja nthawi imeneyo nʼkuti utabadwa kale!
Wakhala ndi moyo zaka zambiridi!
22 “Kodi unalowamo mʼnyumba zosungira chisanu chowundana
kapena unayionapo nyumba yosungira matalala,
23 zimene ndazisungira nthawi ya mavuto
ndi nthawi yomenyana ndi ya nkhondo?
24 Kodi umadziwa njira ya kumene kumachokera chingʼaningʼani
kapena njira ya kumene kumachokera mphepo ya kummawa imene ili pa dziko lonse lapansi?
25 Kodi ndani amene amakonza ngalande za mvula,
nanga ndani anakonza njira yoyendamo mphenzi,
26 kuthirira madzi dziko limene sikukhala munthu,
chipululu chopandamo munthu,
27 kukhutitsa nthaka yowuma yagwaa
ndi kumeretsamo udzu?
28 Kodi mvula ili ndi abambo ake?
Nanga madzi a mame anawabereka ndani?
29 Kodi madzi owundana anawabereka ndani?
Ndani amene anabereka chisanu chochokera kumwamba
30 pamene madzi amawuma gwaa ngati mwala,
pamene madzi a pa nyanja amazizira, nalimba kuti gwaa?
31 “Kodi iwe ungayimitse kuyenda kwa nyenyezi?
Kodi ungathe kuletsa kuyenda kwa nsangwe ndi akamwiniatsatana?
32 Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yake
kapena kutsogolera nyenyezi yayikulu ya chimbalangondo pamodzi ndi ana ake?
33 Kodi malamulo a mlengalenga umawadziwa?
Kodi ungathe kukhazikitsa ulamuliro wa Mulungu pa dziko lapansi?
34 “Kodi iwe ungathe kulamula mitambo
kuti igwetse mvula ya chigumula?
35 Kodi ungathe kutumiza zingʼaningʼani kuti zingʼanime?
Kodi zimabwera pamaso pako ndi kuti, ‘Tili pano?’
36 Kodi ndani anayika nzeru mu mtima,
ndani analonga mʼmaganizo nzeru zomvetsa zinthu?
37 Wanzeru ndani amene angathe kuwerenga mitambo?
Ndani angathe kupendeketsa mitsuko ya madzi akuthambo
38 pamene fumbi limasanduka matope,
ndipo matopewo amawumbika?
39 “Kodi ndani amawusakira chakudya mkango waukazi
ndi kukhutitsa misona ya mikango
40 pamene ili khale mʼmapanga mwawo
kapena pamene ikubisala pa tchire?
41 Kodi amamupatsa khwangwala chakudya chake ndani
pamene ana ake akulirira kwa Mulungu
ndi kumayendayenda chifukwa chosowa zakudya?
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.