Yobu 10
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
10 “Ine ndatopa nawo moyo wanga;
choncho ndidzanena zodandaula zanga momasuka
ndipo ndidzayankhula mwa kuwawidwa mtima kwanga.
2 Ndidzati kwa Mulungu wanga: Musandiweruze kuti ndine wolakwa,
koma mundiwuze chifukwa chimene Inu mukukanganira ndi ine.
3 Kodi mumakondwera mukamandizunza,
kunyoza ntchito ya manja anu,
chonsecho mukusekerera ndi zochita za anthu oyipa?
4 Kodi maso anu ali ngati a munthu?
Kodi mumaona zinthu monga momwe amazionera munthu?
5 Kodi masiku anu ali ngati masiku a munthu,
kapena zaka zanu ngati zaka za munthu,
6 kuti Inu mufufuze zolakwa zanga
ndi kulondola tchimo langa,
7 ngakhale mukudziwa kuti sindine wolakwa
ndiponso kuti palibe amene angandilanditse mʼdzanja lanu?
8 “Munandiwumba ndi kundipanga ndi manja anu.
Kodi tsopano Inu mudzatembenuka ndi kundiwononga?
9 Kumbukirani kuti munandipanga ndi dothi,
kodi tsopano mundibwezeranso ku fumbi?
10 Suja munapatsa abambo anga mphamvu zoti andibale,
suja munandikuza bwino mʼmimba mwa amayi anga?
11 Munandikuta ndi khungu ndi mnofu
ndi kundilumikiza pamodzi ndi mafupa ndi mitsempha?
12 Munandipatsa moyo ndi kundionetsa chifundo chanu,
ndipo munasamalira bwino moyo wanga.
13 “Koma izi ndi zimene munabisa mu mtima mwanu,
ndipo ndikudziwa kuti zinali mʼmaganizo anu:
14 Kuti ngati ndingachimwe mudzakhala mukundipenyetsetsa
ndipo kuti simudzalola kuti ndisalangidwe chifukwa cha kulakwa kwanga.
15 Ngati ndili wolakwa, tsoka langa!
Koma ngakhale ndili wosalakwa sindingathe kutukula mutu wanga,
pakuti ndagwidwa ndi manyazi
ndipo ndamizidwa mʼmavuto anga.
16 Ndipo ndikatukula mutu wanga, Inu mumandisaka ngati mkango
ndiponso mumandiopseza ndi mphamvu yanu.
17 Mumabweretsa mboni zatsopano potsutsana nane
ndipo mkwiyo wanu pa ine umanka nukulirakulira ndi
magulu anu olimbana nane amanka nachulukirachulukira.
18 “Chifukwa chiyani Inu munalola kuti ndibadwe?
Ndi bwino ndikanafa diso lililonse lisanandione.
19 Ndikanapanda kubadwa,
kapena akanangonditenga nditabadwa kupita nane ku manda!
20 Kodi masiku anga owerengeka sali pafupi kutha?
Ndilekeni kuti ndipumule pangʼono pokha
21 ndisanapite ku malo amene munthu sabwererako
ku dziko la imfa ndi kwa mdima wandiweyani,
22 ku dziko la mdima wandiweyani
ndi chisokonezo,
kumene kuwala kumakhala ngati mdima.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.