Yesaya 64
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
64 Inu Yehova, bwanji mukanangongʼamba mlengalenga ndi kutsika pansi,
kuti mapiri agwedezeke pamaso panu!
2 Monga momwe moto umatenthera tchire
ndiponso kuwiritsa madzi,
tsikani kuti adani anu adziwe dzina lanu,
ndiponso kuti mitundu ya anthu injenjemere pamaso panu.
3 Pakuti nthawi ina pamene munatsika munachita zinthu zoopsa zimene sitinaziyembekezere,
ndipo mapiri anagwedezeka pamaso panu.
4 Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe anamvapo
kapena kuona
Mulungu wina wonga Inu,
amene amachitira zinthu zotere amene amadikira pa Iye.
5 Inu mumabwera kudzathandiza onse amene amakondwera pochita zolungama,
amene amakumbukira njira zanu.
Koma Inu munakwiya,
ife tinapitiriza kuchimwa.
Kodi nanga tingapulumutsidwe bwanji?
6 Tonsefe takhala ngati anthu amene ndi odetsedwa,
ndipo ntchito zathu zili ngati sanza za msambo;
tonse tafota ngati tsamba,
ndipo machimo athu akutiwuluzira kutali ngati mphepo.
7 Palibe amene amapemphera kwa Inu
kutekeseka kuti apemphe chithandizo kwa Inu;
pakuti mwatifulatira
ndi kutisiya chifukwa cha machimo athu.
8 Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu.
Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba;
ife tonse ndi ntchito ya manja anu.
9 Inu Yehova, musatikwiyire kopitirira muyeso
musakumbukire machimo athu mpaka muyaya.
Chonde, mutiganizire, ife tikupempha,
pakuti tonsefe ndi anthu anu.
10 Mizinda yanu yopatulika yasanduka chipululu;
ngakhaletu Ziyoni wasanduka chipululu, Yerusalemu ndi wamasiye.
11 Nyumba yanu yopatulika ndi yaulemu, kumene makolo athu ankakutamandani,
yatenthedwa ndi moto
ndipo malo onse amene tinkawakonda asanduka bwinja.
12 Inu Yehova, zonse zachitikazi, kodi mungokhala osatithandiza?
Kodi mudzapitirizabe kukhala chete ndi kutilangabe mopitirira muyeso?
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.