Yesaya 22
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Za Chilango cha Yerusalemu
22 Uthenga wonena za Chigwa cha Masomphenya:
Kodi chachitika nʼchiyani,
kuti nonsenu mukwere pa madenga?
2 Iwe mzinda wodzaza ndi chisangalalo chodzaza tsaya,
iwe mzinda waphokoso ndi wosokonekera?
Anthu ako ophedwa aja sanaphedwe ndi lupanga,
kapena kufera pa nkhondo.
3 Atsogoleri ako onse ngakhale anathawa limodzi;
koma anagwidwa osadziteteza nʼkomwe.
Inu munapezeka ndipo nonse pamodzi munatengedwa ukapolo,
ngakhale munathawa pamene mdani akanali patali.
4 Nʼchifukwa chake Ine ndinati, “Chokani pamaso panga;
ndilekeni ndilire ndi mtima wowawa.
Musayesere kunditonthoza
chifukwa cha kuwonongeka kwa anthu anga.”
5 Lero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse walola kuti tione
mavuto ndi kugonjetsedwa ndiponso chisokonezo
mʼChigwa cha Masomphenya.
Malinga agumuka,
komanso anthu akanalira mofuwula ku mapiri.
6 Ankhondo a ku Elamu anadza pa magaleta
ndi akavalo ali ndi mivi mʼmanja.
Ankhondo a ku Kiri anakonzeka ndi zishango.
7 Zigwa zanu zachonde ndi zodzaza ndi magaleta,
ndipo asilikali okwera pa akavalo ayikidwa pa zipata za mzinda;
8 zonse zoteteza Yuda zachotsedwa.
Ndipo tsiku limenelo munayangʼanayangʼana
zida zankhondo zomwe zinali mʼnyumba yaufumu ya nkhalango;
9 inu munaona kuti makoma ambiri a mzinda wa Davide
anali ndi malo ambiri ogumuka;
munasunga madzi
mu chidziwe chakumunsi.
10 Munawerenga nyumba zonse za mu Yerusalemu
ndipo munagwetsa nyumba zina kuti mulimbitse linga logumuka lija.
11 Pakati pa makoma awiri munamanga chitsime
chosungiramo madzi ochokera ku dziwe lakale,
koma inu simunadalire Mulungu amene anapanga zimenezi,
kapena kusamalako za Iye amene anazilenga kale lomwe.
12 Pa tsiku limenelo, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse
anakuyitanani kuti mulire ndi kukhetsa misozi;
kumeta mutu wanu mpala
ndi kuvala ziguduli.
13 Koma mʼmalo mwake inu munakondwa ndi kusangalala;
munapha ngʼombe ndi nkhosa;
munadya nyama ndi kumwa vinyo.
Inu mumati, “Tiyeni tidye ndi kumwa
pakuti mawa tifa!”
14 Yehova Wamphamvuzonse wandiwululira mondinongʼoneza kuti, “Tchimo limeneli sindidzakhululuka mpaka tsiku la kufa kwanu,” akutero Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse.
15 Chimene Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Pita, ukanene kwa Sabina kapitawo,
amene amayangʼanira nyumba yaufumu:
16 Kodi ukuchita chiyani kuno, nanga ndani anakupatsa chilolezo
kuti udzikumbire manda kuno,
kudzikumbira manda pa phiri
ndi kudzisemera malo opumulira mʼthanthwe?
17 “Samalira, Yehova watsala pangʼono kukugwira zolimba
ndi kukuponya mwamphamvu, iwe munthu wamphamvu.
18 Iye adzakukulunga kwambiri ngati mpira
ndipo adzakuponyera mʼdziko lalikulu.
Kumeneko ndiko ukafere
ndipo kumeneko ndiko kudzatsalire magaleta ako.
Ndipo udzasanduka wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wako.
19 Ine ndidzakuchotsa pa ukapitawo wako
ndipo ndidzakutsitsa pa udindo wako.
20 “Tsiku limenelo ndidzayitanitsa mtumiki wanga, Eliyakimu mwana wa Hilikiya. 21 Ndidzamuveka mkanjo wako ndi kumangira lamba wako mʼchiwuno mwake ndi kumupatsa ulamuliro wako. Iye adzakhala kholo la amene amakhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda. 22 Ndidzamupatsa ulamuliro wa banja la Davide. Adzatsekula ndipo palibe adzatseke, adzatseka popanda wina kutsekula. 23 Ufumu wake udzakhala wokhazikika ngati chikhomo chokhomedwa pa malo olimba. Anthu adzalemekeza nyumba ya abale ake chifukwa cha iye. 24 Ana ndi abale a nyumba ya abambo ake adzakhala ngati katundu pa iye ngati ziwiya zopanda ntchito zimene zapachikidwa pa chikhomo.
25 “Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Tsiku limeneli chikhomo chokhomedwa kwambiri chija sichidzalimbanso; chidzazuka ndipo chidzagwa ndipo zonse zopachikidwa zidzawonongedwa.’ ” Yehova wayankhula chomwechi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.