Nyimbo ya Solomoni 5
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mwamuna
5 Ndalowa mʼmunda mwanga, iwe mlongo wanga, iwe mkwatibwi wanga;
ndasonkhanitsa mure wanga ndi zokometsera zakudya zanga.
Ndadya uchi wanga pamodzi ndi zisa zake zomwe;
ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga.
Abwenzi
Idyani abwenzi anga, imwani;
Inu okondana, imwani kwambiri.
Mkazi
2 Ndinagona tulo koma mtima wanga unali maso.
Tamverani, bwenzi langa akugogoda:
“Nditsekulire, mlongo wanga, bwenzi langa,
nkhunda yanga, wangwiro wanga.
Mutu wanga wanyowa ndi mame,
tsitsi langa lanyowa chifukwa cha nkhungu ya usiku.”
3 Ndavula kale zovala zanga,
kodi ndizivalenso?
Ndasamba kale mapazi anga
kodi ndiwadetsenso?
4 Bwenzi langa anapisa dzanja lake pa chibowo cha pa chitseko;
mtima wanga unagunda chifukwa cha iye.
5 Ndinanyamuka kukamutsekulira wachikondi wangayo,
ndipo manja anga anali noninoni ndi mure,
zala zanga zinali mure chuchuchu,
pa zogwirira za chotsekera.
6 Ndinamutsekulira wachikondi wanga,
koma nʼkuti wachikondi wangayo atachoka; iye anali atapita.
Mtima wanga unafumuka chifukwa cha kuchoka kwake.
Ndinamuyangʼanayangʼana koma sindinamupeze.
Ndinamuyitana koma sanandiyankhe.
7 Alonda anandipeza
pamene ankayendera mzindawo.
Anandimenya ndipo anandipweteka;
iwo anandilanda mwinjiro wanga,
alonda a pa khoma aja!
8 Inu akazi a ku Yerusalemu ndithu ndikukupemphani,
mukapeza wokondedwa wangayo,
kodi mudzamuwuza chiyani?
Muwuzeni kuti ine ndadwala nacho chikondi.
Abwenzi
9 Iwe wokongola kuposa akazi onsewa,
kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana wina aliyense bwanji?
Kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana ena onse chotani
kuti uzichita kutipempha motere?
Mkazi
10 Wokondedwa wangayo ndi wowala kwambiri ndi wathanzi
pakati pa anthu 1,000.
11 Mutu wake ndi golide woyengeka bwino;
tsitsi lake ndi lopotanapotana,
ndiponso lakuda bwino ngati khwangwala.
12 Maso ake ali ngati nkhunda
mʼmbali mwa mitsinje ya madzi,
ngati nkhunda zitasamba mu mkaka,
zitayima ngati miyala yamtengowapatali.
13 Masaya ake ali ngati timinda ta mbewu zokometsera zakudya
zopatsa fungo lokoma.
Milomo yake ili ngati maluwa okongola
amene akuchucha mure.
14 Manja ake ali ngati ndodo zagolide
zokongoletsedwa ndi miyala yamtengowapatali.
Thupi lake ndi losalala ngati mnyanga wanjovu
woyikamo miyala ya safiro.
15 Miyendo yake ili ngati mizati yamwala,
yokhazikika pa maziko a golide.
Maonekedwe ake ali ngati Lebanoni,
abwino kwambiri ngati mkungudza.
16 Milomo yake ndi yosangalatsa kwambiri;
munthuyo ndi wokongola kwambiri!
Uyu ndiye wachikondi wanga ndi bwenzi langa,
inu akazi a ku Yerusalemu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.