Numeri 25
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Aisraeli Achita Chigololo
25 Aisraeli akukhala ku Sitimu, anayamba kuchita chigololo ndi akazi a ku Mowabu, 2 amene ankawayitana ku nsembe za milungu yawo. Anthuwo anadya chakudya chopereka kwa milungu ndi kupembedza milunguyo. 3 Motero Aisraeli anapembedza nawo Baala-Peori ndipo Yehova anawapsera mtima kwambiri.
4 Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Tenga atsogoleri onse a anthu awa, uwaphe poyera, pamaso pa Yehova kuti mkwiyo waukulu wa Yehova uchoke pa Israeli.”
5 Choncho Mose anawuza oweruza a Israeli kuti, “Aliyense wa inu ayenera kupha anthu ake amene anapembedza nawo Baala-Peori.”
6 Kenaka mwamuna wina wa ku Israeli anabweretsa ku banja lake mkazi wa Chimidiyani pamaso pa Mose ndi anthu onse a Israeli pamene ankalira pa khomo la tenti ya msonkhano. 7 Finehasi mwana wa Eliezara, mwana wa wansembe Aaroni ataona izi, anachoka pa msonkhanowo, natenga mkondo mʼdzanja lake. 8 Ndipo anatsatira Mwisraeliyu mpaka mʼtenti yake. Anasolola mkondowo ndi kubaya awiriwo kupyola Mwisraeliyo mpaka mʼthupi la mkaziyo. Pamenepo mliri unaleka pakati pa Aisraeli. 9 Pa mliriwo, anthu okwana 24,000 anafa.
10 Yehova anawuza Mose kuti, 11 “Finehasi mwana wa Eliezara, mwana wa wansembe Aaroni wabweza mkwiyo wanga pa Aisraeli chifukwa sanalole kuti wina aliyense apembedze mulungu wina koma Ine ndekha. Nʼchifukwa chake sindinawawononge mu mkwiyo wanga. 12 Tsono muwuze kuti ndikhazikitsa pangano langa la mtendere ndi iye. 13 Ndikupangana naye pangano la unsembe wosatha, iyeyo pamodzi ndi zidzukulu zake zonse, chifukwa sanalole kuti anthu awukire Ine Mulungu, ndipo anachita ntchito yopepesera machimo Aisraeli.”
14 Dzina la Mwisraeli yemwe anaphedwa ndi mkazi wa Chimidiyani anali Zimuri mwana wa Salu, mtsogoleri wa banja la Simeoni. 15 Ndipo dzina la mkazi wa Chimidiyani, yemwe anaphedwayo, linali Kozibi mwana wa Zuri, mtsogoleri wa fuko la ku Midiyaniko.
16 Yehova anawuza Mose kuti, 17 “Amidiyani ndi adani anu ndipo uwaphe, 18 chifukwa ankakuonani inu ngati adani awo pamene anakupusitsani pa nkhani ya ku Peori, ndiponso za mlongo wawo Kozibi, mwana wamkazi wa mtsogoleri wa Amidiyani, mkazi yemwe anaphedwa pamene mliri unabwera chifukwa cha zimene zinachitika ku Peori.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.