Numeri 23
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Uthenga Woyamba wa Balaamu
23 Balaamu anati kwa Balaki, “Mundimangire maguwa ansembe asanu ndi awiri pano, ndipo mukonzenso ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri.” 2 Balaki anachita monga Balaamu ananenera ndipo awiriwo anapereka ngʼombe imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzi pa guwa lansembe lililonse.
3 Kenaka Balaamu anati kwa Balaki, “Khalani pano pafupi ndi nsembe yanu ineyo ndipite pambali. Mwina Yehova adzabwera kuti akumane nane. Chilichonse chimene akandionetse ndidzakuwuzani” Choncho anapita ku malo okwera a chipululu.
4 Mulungu anakumana naye ndipo Balaamu anati, “Ndakonza maguwa asanu ndi awiri ndipo pa guwa lililonse ndaperekapo nsembe ya ngʼombe yayimuna imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzinso.”
5 Yehova anawuza Balaamu kuti, “Bwerera kwa Balaki ndipo ukamuwuze uthenga uwu.”
6 Ndipo anabwerera kwa iye namupeza atayima pafupi ndi nsembe yake pamodzi ndi akuluakulu onse a Mowabu. 7 Ndipo Balaamu ananena uthenga wake:
“Balaki ananditenga kuchoka ku Aramu,
mfumu ya ku Mowabu kuchokera ku mapiri a kummawa.
Iye anati, ‘Bwera, temberera Yakobo mʼmalo mwanga,
pita nyoza Israeli.’
8 Ndingatemberere bwanji
amene Mulungu sanawatemberere?
Ndinganyoze bwanji
amene Yehova sanawanyoze?
9 Kuchokera pamwamba pa mapiri ndikuona anthu,
ndikuwaona kuchokera pa zitunda.
Ndikuona anthu okhala pawokha,
osakhala mʼgulu limodzi ndi mitundu ina.
10 Ndani angawerenge zidzukulu za Yakobo zochuluka ngati fumbi,
kapena chimodzi mwa zigawo zinayi za Israeli?
Lekeni ndife imfa ya oyera mtima,
ndi chimaliziro changa chikhale ngati chawo!”
11 Balaki anati kwa Balaamu, “Wandichitira chiyani? Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, ndipo taona, sunachite chilichonse koma kuwadalitsa!”
12 Iye anayankha kuti, “Kodi sindinayenera kuyankhula zimene Yehova anandiwuza?”
Uthenga Wachiwiri wa Balaamu
13 Kenaka Balaki anawuza Balaamu kuti, “Tiye tipite limodzi ku malo ena komwe ungawaone. Udzangoona gulu limodzi osati onsewo. Ndipo pamenepo, ukawatemberere mʼmalo mwanga.” 14 Tsono anamutengera ku munda wa Zofimu pamwamba pa phiri la Pisiga ndipo kumeneko anamanga maguwa ansembe asanu ndi awiri ndipo anapereka nsembe ngʼombe yayimuna imodzi ndi nkhosa yayimuna imodzi pa guwa lansembe lililonse.
15 Balaamu anawuza Balaki kuti, “Khalani pano pafupi ndi nsembe yanu pamene ine ndikukakumana ndi Mulungu cha uko.”
16 Yehova anakumana ndi Balaamu ndipo anamuyankhula kuti, “Bwerera kwa Balaki ndipo ukamuwuze uthenga uwu.”
17 Ndipo anapita kwa iye ndipo anamupeza atayimirira pafupi ndi nsembe yake pamodzi ndi akuluakulu a ku Mowabu. Balaki anafunsa Balaamu kuti, “Yehova wayankhula chiyani?”
18 Pamenepo Balaamu ananena uthenga wake:
“Nyamuka Balaki ndipo tamvera;
Undimvere iwe mwana wa Zipori.
19 Mulungu si munthu kuti aname,
kapena mwana wa munthu kuti asinthe maganizo ake.
Kodi amayankhula koma osachita?
Kodi amalonjeza koma osakwaniritsa?
20 Wandilamula kuti ndidalitse,
Iyeyo wadalitsa ndipo sindingasinthe.
21 “Palibe kuwukira kulikonse kumene wakuona mwa Yakobo,
sanaone chovuta mu Israeli.
Yehova Mulungu wawo ali nawo:
mfuwu wa mfumu uli pakati pawo.
22 Mulungu wowatulutsa mʼdziko la Igupto,
ali ndi mphamvu ngati za njati.
23 Palibe matsenga amene angalimbane ndi Yakobo,
palibe mawula amene angalimbane ndi Israeli.
Tsopano za Yakobo ndi Israeli adzanena kuti,
‘Onani zimene Mulungu wachita!’
24 Taonani, anthu anyamuka ngati mkango waukazi;
adzuka okha ngati mkango waumuna
umene supuma mpaka utadya nyama imene wagwira
ndi kumwa magazi a nyama yogwidwayo.”
25 Ndipo Balaki anati kwa Balaamu, “Usawatemberere ndi pangʼono pomwe kapena kuwadalitsa!
26 “Balaamu anayankha Balaki kuti, ‘Kodi sindinakuwuzeni kuti ndiyenera kuchita zimene Yehova wanena?’ ”
Uthenga Wachitatu wa Balaamu
27 Kenaka Balaki anati kwa Balaamu, “Bwera ndikutengere ku malo ena. Mwina chidzamukondweretsa Mulungu kuti uwatemberere kumeneko mʼmalo mwanga.” 28 Ndipo Balaki anamutengera Balaamu pamwamba pa Peori, poyangʼanana ndi chipululu.
29 Balaamu anati kwa Balaki, “Mundimangire maguwa ansembe asanu ndi awiri pano ndipo mundikonzere ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri.” 30 Balaki anachita monga Balaamu ananenera ndipo anapereka nsembe ngʼombe imodzi yayimuna ndi nkhosa imodzi yayimuna pa guwa lililonse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.