Nahumu 3
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Tsoka la Ninive
3 Tsoka kwa mzinda wopha anthu,
mzinda wodzaza ndi mabodza,
mzinda wodzaza ndi anthu olanda zinthu anzawo,
mu mzinda mʼmene simusowa anthu osautsidwa nthawi zonse!
2 Kulira kwa zikwapu,
mkokomo wa mikombero,
kufuwula kwa akavalo
ndiponso phokoso la magaleta!
3 Kuthamanga kwa anthu okwera pa akavalo,
kungʼanima kwa malupanga
ndi kunyezimira kwa mikondo!
Anthu ambiri ophedwa,
milumilu ya anthu akufa,
mitembo yosawerengeka,
anthu akupunthwa pa mitemboyo.
4 Zonsezi ndi chifukwa cha zilakolako za mkazi wachiwerewere,
wokopa anthu uja, mkazi wochita zamatsenga,
amene anakopa mitundu ya anthu ndi zachiwerewere zake,
ndiponso anthu a mitundu ina ndi zaufiti zake.
5 Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Ine ndikutsutsana nawe.
Ndidzakuvula chovala chako.
Anthu a mitundu ina ndidzawaonetsa umaliseche wako
ndipo udzachita manyazi pamaso pa maufumu onse.
6 Ndidzakuthira zonyansa,
ndidzakuchititsa manyazi
ndiponso kukusandutsa chinthu choseketsa.
7 Onse amene adzakuona adzakuthawa ndipo adzati,
‘Ninive wasanduka bwinja,
adzamulira ndani?’
Kodi ndingamupeze kuti munthu woti nʼkukutonthoza?”
8 Kodi ndiwe wopambana Tebesi,
mzinda wokhala mʼmbali mwa Nailo,
wozunguliridwa ndi madzi?
Mtsinjewo unali chitetezo chake,
madziwo anali linga lake.
9 Mphamvu zake zinali Kusi ndi Igupto,
Puti ndi Libiya anali ena mwa abwenzi ake.
10 Komabe anthu a ku Tebesi anagwidwa
ndipo anapita ku ukapolo.
Ana ake anawaphwanyitsa pansi
mʼmisewu yonse ya mu mzindamo.
Anachita maere ogawana anthu ake otchuka,
ndipo anthu ake onse amphamvu
anamangidwa ndi maunyolo.
11 Iwenso Ninive udzaledzera;
udzabisala
ndipo udzafunafuna malo othawirako kuopa mdani.
12 Malo ako onse otetezedwa ali ngati mitengo ya mkuyu
yokhala ndi zipatso zoyambirira kucha;
pamene agwedeza mitengoyo,
nkhuyuzo zimagwera mʼkamwa mwa wofuna kuzidya.
13 Tayangʼana ankhondo ako,
onse ali ngati akazi!
Zipata za dziko lako zatsekukira adani ako;
moto wapsereza mipiringidzo yake.
14 Tungani madzi woti mudzamwe nthawi ya kuzunguliridwa kwanu,
limbitsani chitetezo chanu!
Pondani dothi,
ikani mʼchikombole,
konzani khoma la njerwa!
15 Kumeneko moto udzakupserezani;
lupanga lidzakukanthani
ndipo lidzakuwonongani ngati likuwononga ziwala.
Chulukanani ngati ziwala,
chulukanani ngati dzombe!
16 Mwachulukitsa chiwerengero cha anthu a malonda anu
mpaka kupambana nyenyezi za mlengalenga,
koma iwo ngati dzombe akuwononga dziko
ndipo kenaka akuwuluka nʼkuchoka.
17 Akalonga ako ali ngati dzombe,
akuluakulu ako ali ngati gulu la dzombe
limene lamatirira pa khoma nthawi yozizira,
koma pamene dzuwa latuluka limawuluka,
ndipo palibe amene amadziwa komwe lapita.
18 Iwe mfumu ya ku Asiriya,
abusa ako agona tulo;
anthu ako olemekezeka amwalira.
Anthu ako amwazikira ku mapiri
popanda ndi mmodzi yemwe wowasonkhanitsa.
19 Palibe chimene chingachize bala lako;
chilonda chako sichingapole.
Aliyense amene amamva za iwe
amawomba mʼmanja chifukwa cha kugwa kwako,
kodi alipo amene sanazilawepo
nkhanza zako zosatha?
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.