Mlaliki 2
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Zosangalatsa Nʼzopandapake
2 Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Tsopano ndiyese zosangalatsa kuti ndipeze zomwe ndi zabwino.” Koma izi zinaonekanso kuti ndi zopandapake. 2 “Kuseka,” ndinati, “imeneyo ndi misala. Ndipo kodi chisangalalo chimabweretsa phindu lanji?” 3 Ndinayesa kudzisangalatsa ndi vinyo, koma umenewu unali uchitsiru, pamenepo nʼkuti maganizo anga akutsogozedwa ndi nzeru. Ine ndinkati mwina kapena njira yotero nʼkukhala yopambana, imene anthu amatsata pofuna kusangalala pa masiku owerengeka a moyo wawo.
4 Ndinagwira ntchito zikuluzikulu: Ndinadzimangira nyumba ndi kuwoka mipesa. 5 Ndinalima madimba ndi minda yamitengo; ndipo ndinadzalamo mitengo ya zipatso za mitundu yonse. 6 Ndinakumba mayiwe osungiramo madzi woti ndizithirira minda ya mitengo yodzalidwa ija. 7 Ndinagula akapolo aamuna ndi akapolo aakazi, ndiponso ndinali ndi akapolo ena omwe anabadwira mʼnyumba mwanga. Ndinalinso ndi ngʼombe ndi nkhosa zambiri kupambana aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. 8 Ndinadzikundikira siliva ndi golide, ndiponso chuma chochokera kwa mafumu ndi madera awo. Ndinali ndi amuna ndi akazi oyimba ndiponso azikazi; zinthu zokondweretsa mtima wa munthu. 9 Ndinali munthu wotchuka kupambana wina aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. Mu zonsezi nzeru zanga zinali nane.
10 Sindinadzimane chilichonse chimene maso anga anachifuna;
mtima wanga sindinawumane zokondweretsa.
Mtima wanga unakondwera ndi ntchito yanga yonse,
ndipo iyi ndiyo inali mphotho ya ntchito zanga zonse zolemetsa.
11 Koma pamene ndinayamba kuyangʼanayangʼana zonse zimene ndinachita ndi manja anga,
ndi zimene ndinazivutikira kuti ndizipeze,
zonsezi zinali zopandapake; kungodzivuta chabe,
palibe chomwe ndinapindula pansi pano.
Nzeru ndi Uchitsiru Nʼzopandapake
12 Kenaka maganizo anga anayamba kulingalira zakuti nzeru nʼchiyani,
komanso kuti misala ndi uchitsiru nʼchiyani.
Kodi munthu wodzalowa ufumu tsopanoyo angachite chiyani
choposa chimene chinachitidwa kale?
13 Ndinaona kuti nzeru ndi yopambana uchitsiru,
monga momwe kuwala kumapambanira mdima.
14 Munthu wanzeru amayenda maso ali patsogolo,
pamene chitsiru chimayenda mʼchimbulimbuli;
koma ndinazindikira kuti chomwe
chimawachitikira onsewo ndi chimodzi.
15 Pamenepo ndinalingalira mu mtima mwanga,
“Zochitikira chitsiru zidzandichitikiranso ine.
Nanga tsono phindu langa nʼchiyani pakukhala wanzeru?”
Ndinati mu mtima mwanga,
“Ichinso ndi chopandapake.”
16 Pakuti munthu wanzeru, pamodzinso ndi chitsiru sadzakumbukiridwa nthawi yayitali;
mʼmasiku amʼtsogolo awiriwo adzayiwalika.
Mmene chimafera chitsiru ndi mmenenso amafera wanzeru!
Kugwira Ntchito Nʼkopandapake
17 Kotero ndinadana nawo moyo chifukwa ntchito zimene zimagwiridwa pansi pano ndi zosautsa kwa ine. Ntchito zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe. 18 Ine ndinadana nazo ntchito zonse zimene ndinazigwira pansi pano, chifukwa ndinayenera kudzazisiyira wina amene adzalowa mʼmalo mwanga. 19 Ndipo ndani amadziwa kuti munthu ameneyo adzakhala wanzeru kapena chitsiru? Komabe munthuyo adzakhala wolamulira zonse zimene ndinazichita pansi pano mwa nzeru zanga. Izinso ndi zopandapake. 20 Motero ndinayamba kutaya mtima chifukwa cha ntchito zonse zimene ndinazivutikira pansi pano. 21 Pakuti munthu atha kugwira ntchito yake mwanzeru, chidziwitso ndi luntha, ndipo kenaka nʼkusiyira wina amene sanakhetserepo thukuta. Izinso ndi zopandapake ndiponso tsoka lalikulu. 22 Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhawa zimene amazichita pansi pano? 23 Masiku ake onse amakhala achisoni, ntchito yake imakhala yovuta; ngakhale usiku womwe, mtima wake supumula. Izinso ndi zopandapake.
24 Kwa munthu palibe chabwino china kuposa kudya, kumwa ndi kukondwerera ntchito zake. Izinso ndaona kuti ndi zochokera kwa Mulungu, 25 pakuti popanda Iye, ndani angadye ndi kupeza chisangalalo? 26 Munthu amene amakondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamusandutsa wanzeru, wozindikira ndi wachisangalalo, koma wochimwa, Mulungu amamupatsa ntchito yosonkhanitsa ndi kusunga chuma kuti adzachipereke kwa amene Mulunguyo amakondwera naye. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.