Mlaliki 11
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Kuponya Chakudya pa Madzi
11 Ponya chakudya chako pa madzi,
udzachipezanso patapita masiku ambiri.
2 Ndalama zako uzisungitse kwa anthu asanu ndi awiri, inde kwa anthu asanu ndi atatu,
pakuti sudziwa ndi tsoka lanji limene likubwera pa dziko.
3 Ngati mitambo yadzaza ndi madzi,
imagwetsa mvula pa dziko lapansi.
Mtengo ukagwera cha kummwera kapena cha kumpoto,
ndiye kuti udzagonera kumene wagwerako.
4 Amene amayangʼana mphepo sadzadzala;
amene amayangʼana mitambo sadzakolola.
5 Momwe sudziwira mayendedwe a mphepo,
kapena momwe mzimu umalowera mʼthupi la mwana mʼmimba mwa amayi,
momwemonso sungathe kudziwa ntchito za Mulungu,
Mlengi wa zinthu zonse.
6 Dzala mbewu zako mmawa
ndipo madzulo usamangoti manja lobodo,
pakuti sudziwa chimene chidzapindula,
mwina ichi kapena icho,
kapena mwina zonse ziwiri zidzachita bwino.
Kumbukira Mlengi Wako
7 Kuwala nʼkwabwino,
ndipo maso amasangalala kuona dzuwa.
8 Munthu akakhala wa zaka zambiri,
mulekeni akondwerere zaka zonsezo,
koma iye azikumbukira masiku a mdima,
pakuti adzakhala ochuluka.
Chilichonse chimene chikubwera ndi chopanda phindu.
9 Kondwera mnyamata iwe, pamene ukanali wamngʼono,
ndipo mtima wako usangalale pa nthawi ya unyamata wako.
Tsatira zimene mtima wako ukufuna,
ndiponso zimene maso ako akuona,
koma dziwa kuti pa zinthu zonsezo
Mulungu adzakuweruza.
10 Choncho uchotse zokusautsa mu mtima mwako,
upewe zokupweteka mʼthupi mwako,
pakuti unyamata ndi ubwana ndi zopandapake.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.