Miyambo 30
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mawu a Aguri
30 Nawa mawu a Aguri mwana wa Yake wa ku Masa:
Munthuyo anati kwa Itieli, “Inu Mulungu, ine ndatopa.
Inu Mulungu, ine ndatopa. Ndalefukiratu.
2 “Ine ndine munthu wopusa kuposa anthu onse;
ndilibe nzeru zomvetsa zinthu zonga za munthu.
3 Sindinaphunzire nzeru,
ndipo Woyerayo sindimudziwa.
4 Kodi ndani anakwera kumwamba ndi kutsikako?
Ndani anafumbatapo mphepo mʼmanja mwake?
Ndani anamanga madzi mʼchovala chake?
Ndani anakhazikitsa mathero onse a dziko lapansi?
Dzina lake ndani? Ndiwuze ngati ukudziwa!
Ndipo mwana wake dzina lake ndani?
5 “Mawu ali wonse a Mulungu ndi opanda cholakwika;
Iye ndi chishango kwa amene amathawira kwa Iye.
6 Usawonjezepo kanthu pa mawu ake,
kuopa kuti Iye angadzakudzudzule ndi kukupeza kuti ndiwe wabodza.”
7 “Inu Yehova, ndikukupemphani zinthu ziwiri
musandimane zimenezo ndisanafe:
8 Choyamba, mundichotsere kutali nane mabodza ndi chinyengo.
Chachiwiri, ndisakhale mʼmphawi kapena munthu wachuma.
Koma muzindidyetsa chakudya chondikwanira tsiku ndi tsiku
9 kuopa kuti ndikakhuta kwambiri ndingayambe kukukanani,
nʼkumanena kuti, ‘Yehova ndiye yaninso?’
Kuopanso kuti ndikakhala wosauka ndingayambe kuba,
potero nʼkuyipitsa dzina la Mulungu wanga.”
10 “Usamusinjirire wantchito kwa mbuye wake
kuopa kuti angakutemberere ndipo iweyo nʼkupezeka wolakwa.”
11 “Alipo ena amene amatemberera abambo awo,
ndipo sadalitsa amayi awo.
12 Pali ena amene amadziyesa okha oyera mtima
komatu sanachotse zoyipa zawo.
13 Pali ena ndi odzitukumula kwambiri,
amene amakweza zikope modzitukumula.
14 Pali ena amene mano awo ali ngati malupanga
ndipo zibwano zawo zili ngati mipeni
moti amadya amphawi ndi kuwachotsa pa dziko lapansi.
Amachotsanso anthu osauka pakati pa anzawo.”
15 “Msundu uli ndi ana aakazi awiri
iwo amalira kuti, ‘Tipatseni! Tipatseni!’ ”
“Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta,
zinthu zinayi zimene sizinena kuti, ‘Takhuta!’
16 Manda, mkazi wosabala,
nthaka yosakhuta madzi
ndiponso moto womangoyakirayakira!”
17 Aliyense amene amanyoza abambo ake,
ndi kunyozera kumvera amayi ake,
makwangwala a ku chigwa adzamukolowola maso
ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.
18 Pali zinthu zitatu zimene zimandidabwitsa,
zinthu zinayi zimene ine sindizimvetsetsa.
19 Ndipo ndi izi: mmene chiwulukira chiwombankhanga mlengalenga;
mmene iyendera njoka pa thanthwe;
mmene chiyendera chombo pa nyanja;
ndiponso mmene mwamuna achitira akakhala ndi namwali.
20 Umu ndi mʼmene mkazi amachitira atachita chigololo:
Atatha kudya ndi kupukuta pakamwa pake
iye amanena kuti “Sindinachite kalikonse kolakwa.”
21 Pali zinthu zitatu zimene zimanjenjemeretsa dziko lapansi,
pali zinthu zinayi zimene dziko lapansi silingathe kuzipirira:
22 Kapolo amene wasanduka mfumu,
chitsiru chimene chakhuta,
23 mkazi wonyozeka akakwatiwa
ndiponso wantchito wamkazi akalanda mwamuna wa mbuye wake.
24 Pali zinthu zinayi zingʼonozingʼono pa dziko lapansi,
komatu ndi zochenjera kwambiri:
25 Nyerere zili ngati anthu opanda mphamvu,
komatu zimasungiratu chakudya chake nthawi ya chilimwe;
26 mbira zili ngati anthu opanda mphamvu
komatu zimakonza pokhalapo pawo mʼmiyala;
27 dzombe lilibe mfumu,
komatu lonse limakhala mʼmagulumagulu poyenda.
28 Buluzi ungathe kumugwira mʼmanja
komatu amapezeka mʼnyumba za mafumu.
29 “Pali zinthu zitatu zimene zimayenda chinyachinya,
pali zinthu zinayi zimene zimayenda monyadira:
30 Mkango umene uli wamphamvu kuposa nyama zonse,
ndipo suthawa kanthu kalikonse.
31 Tambala woyenda chinyachinya, mbuzi yayimuna,
ndiponso mfumu yoyenda pakati pa anthu ake.
32 “Ngati wakhala ukupusa ndi kumadzikweza wekha,
kapena ngati wakhala ukukonzekera zoyipa,
ndiye khala kaye chete, uganizire bwino!
33 Paja pakutha mkaka mafuta amapangidwa,
ndipo ukapsinya mphuno, magazi amatuluka,
ndipo mikangano imakhalapo ukalimbikira kukwiya.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.