Miyambo 19
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
19 Ndi wabwino munthu wosauka amene amayenda mu ungwiro,
aposa munthu wopusa woyankhula zokhota.
2 Si bwino kuti munthu akhale wopanda nzeru;
ndipo munthu woyenda mofulumira amaphonya njira.
3 Uchitsiru wa munthu umamubweretsera zovuta,
mtima wake umakwiyira Yehova.
4 Chuma chimachulukitsa abwenzi;
koma munthu wosauka bwenzi lake limamuthawa.
5 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa;
ndipo iye amene amanena mabodza sadzapulumuka.
6 Anthu ambiri amafuna munthu wopatsa kuti awakomere mtima,
ndipo munthu amene amapereka mphatso ndi bwenzi la munthu aliyense.
7 Ngati munthu wosauka abale ake omwe amadana naye,
nanji abwenzi ake tsono!
Iwo adzamuthawa kupita kutali.
Amayesa kuwatsatira mowapembedza koma iwo samapezeka konse.
8 Iye amene amapeza nzeru ndiye kuti amakonda moyo wake.
Wosamalitsa kukhala wanzeru, zinthu zimamuyendera bwino.
9 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,
ndipo iye amene amanena mabodza adzawonongeka.
10 Nʼkosayenera kuti chitsiru chizikhala ndi moyo wamanyado,
nanjinso kuti kapolo azilamulira akalonga!
11 Nzeru zimapangitsa munthu kukhala wosakwiya msanga;
ulemerero wake uli posalabadira kuchitiridwa zoyipa.
12 Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango,
koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pa udzu.
13 Mwana wopusa ndiye tsoka la abambo ake
ndipo mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula yamvumbi.
14 Nyumba ndi chuma ndiye cholowa chochokera kwa makolo;
koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Yehova.
15 Ulesi umagonetsa tulo tofa nato
ndipo munthu wosatakataka amakhala ndi njala.
16 Amene amamvera malangizo amasunga moyo wake,
koma amene sasamala malamulo a Yehova adzafa.
17 Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova,
ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.
18 Langa mwana wako, chiyembekezo chikanalipo;
ngati sutero udzawononga moyo wake.
19 Munthu waukali woopsa ayenera kulandira chilango;
pakuti akamulekelera ndiye zidzayipa kuposa kale.
20 Mvera uphungu ndipo landira malangizo;
pa mapeto pake udzakhala wanzeru.
21 Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake,
koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike.
22 Chimene munthu amafuna ndi chikondi chosatha;
nʼkwabwino kukhala wosauka kusiyana ndi kukhala wabodza.
23 Kuopa Yehova kumabweretsa moyo;
wotereyo amakhala mu mtendere; ndiye kuti choyipa sichidzamugwera.
24 Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale;
koma sangathe kufikitsa dzanja lakelo pakamwa pake.
25 Menya munthu wonyoza, ndipo anthu opanda nzeru adzachenjererapo;
dzudzula munthu wozindikira zinthu, ndipo iye adzapezapo chidziwitso.
26 Mwana wochita ndewu ndi abambo ake ndi kuthamangitsa amayi ake,
ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.
27 Mwana wanga, ukaleka kumvera malangizo,
udzapatukana ndi mawu opatsa nzeru.
28 Mboni yopanda pake imanyoza cholungama,
ndipo pakamwa pa anthu oyipa pamameza zoyipa.
29 Chilango chakonzedwa kale kuti chigwere anthu oyipa,
ndipo mkwapulo wakonzedwa kale kuti ukwapule misana ya anthu opusa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.