Mateyu 17
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Maonekedwe Aulemerero a Yesu pa Phiri
17 Patapita masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo, ndi Yohane mʼbale wa Yakobo pa okha ndipo anakwera nawo pa phiri lalitali. 2 Pamenepo Iye anasinthika maonekedwe ake pamaso pawo. Nkhope yake inawala ngati dzuwa ndipo zovala zake zinayera kuti mbuu. 3 Nthawi yomweyo Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo akuyankhulana ndi Yesu.
4 Petro anati kwa Yesu, “Ambuye ndi bwino kuti ife tikhale pano. Ngati mufuna ndidzamanga misasa itatu umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.”
5 Iye akuyankhulabe, mtambo owala unawaphimba, ndipo mawu ochokera mu mtambo anati, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimukonda ndipo ndikondwera naye kwambiri. Mumumvere Iye!”
6 Ophunzira atamva zimenezi, anachita mantha nagwa pansi chafufumimba. 7 Ndipo Yesu anabwera nawakhudza nati, “Dzukani, musaope.” 8 Atayangʼana, sanaone wina aliyense kupatula Yesu yekha.
9 Akutsika ku phiriko, Yesu anawalamula kuti, “Musawuze wina aliyense zimene mwaona, mpaka Mwana wa Munthu ataukitsidwa kwa akufa.”
10 Ophunzira anamufunsa Iye kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kukhala woyamba kubwera?”
11 Yesu anayankha kuti, “Kunena zoona, Eliya adzayenera kubwera ndipo adzakonza zinthu zonse. 12 Koma Ine ndikuwuzani inu kuti Eliya anabwera kale koma iwo sanamuzindikire ndipo anachita naye chilichonse chimene anafuna. Momwemonso iwo adzazunza Mwana wa Munthu.” 13 Pamenepo ophunzira anazindikira kuti amawawuza za Yohane Mʼbatizi.
Yesu Achiritsa Wodwala Matenda Akugwa
14 Atafika ku gulu la anthu, munthu wina anamuyandikira Yesu ndi kugwada pamaso pake. 15 Iye anati, “Ambuye, muchitireni chifundo mwana wanga akudwala matenda akugwa ndipo akuvutika kwambiri. Kawirikawiri iye amagwa pa moto kapena mʼmadzi. 16 Ine ndinabwera naye kwa ophunzira anu koma alephera kumuchiritsa.”
17 Yesu anayankha nati, “Haa, mʼbado wosakhulupirira ndi wokhota maganizo! Kodi ndidzakhala nanu mpaka liti? Ndidzapirira nanu mpaka liti? Bwera nayeni kwa Ine mnyamatayo.” 18 Yesu anadzudzula chiwandacho ndipo chinatuluka mwa mnyamatayo ndipo anachira nthawi yomweyo.
19 Pamenepo ophunzira anabwera kwa Yesu mwamseri ndi kumufunsa kuti, “Chifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwandacho?”
20 Iye anayankha kuti, “Chifukwa inu muli ndi chikhulupiriro chachingʼono. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, mukhoza kunena ndi phiri ili kuti, ‘Choka apa nupite apo,’ ndipo lidzachoka. Palibe kanthu kamene kadzakukanikani. 21 Chiwanda cha mtundu uwu sichingachoke chabe koma ndi pemphero ndi kusala kudya.”
Yesu Anena za Imfa yake Kachiwiri
22 Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Iye anawawuza kuti, “Mwana wa Munthu akupita kukaperekedwa mʼmanja mwa anthu. 23 Iwo adzamupha koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.” Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chisoni.
Yesu Apereka Msonkho
24 Yesu ndi ophunzira ake atafika ku Kaperenawo, wolandira msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu anabwera kwa Petro namufunsa kuti, “Kodi aphunzitsi anu sapereka msonkho wa Nyumba ya Mulungu?”
25 Iye anayankha kuti, “Inde amapereka.”
Petro atalowa mʼnyumba, Yesu ndiye anayamba kuyankhula. Ndipo anamufunsa kuti, “Ukuganiza bwanji Simoni, kodi mafumu a dziko lapansi amalandira msonkho kuchokera kwa ana awo kapena kwa ena?”
26 Petro anayankha kuti, “Kuchokera kwa ena.”
Yesu ananena kwa iye kuti, “Ndiye kuti ana sapereka.” 27 Koma kuti ife tisawakhumudwitse pita ku nyanja kaponye mbedza yako. Katenge nsomba imene ukayambe kuyikola; kayitsekule kukamwa ndipo ukapezamo ndalama. Katenge ndalamayo ndi kukapereka msonkho wanga ndi wanu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.