Masalimo 77
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Asafu.
77 Ndinafuwulira Mulungu kupempha thandizo;
ndinafuwula mokweza kwa Mulungu kuti anditcherere khutu.
2 Pamene ndinali pa masautso ndinafunafuna Ambuye;
usiku ndinatambasula manja mosalekeza
ndipo moyo wanga unakana kutonthozedwa.
3 Ndinakumbukira Inu Mulungu, ndipo ndinabuwula;
ndinasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unalefuka.
Sela
4 Munagwira zikope zanga kuti ndisagone
ndipo ndinavutika kwambiri kuti ndiyankhule.
5 Ndinaganizira za masiku akale,
zaka zamakedzana;
6 Ndinakumbukira nyimbo zanga usiku.
Mtima wanga unasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unafunsa kuti,
7 “Kodi Ambuye adzatikana mpaka muyaya?
Kodi Iwo sadzaonetsanso kukoma mtima kwawo?
8 Kodi Chikondi chake chosatha chija chatheratu?
Kodi malonjezo ake alephera nthawi yonse?
9 Kodi Mulungu wayiwala kukhala wokoma mtima?
Kodi mu mkwiyo wake waleka chifundo chake?”
10 Ndipo ndinaganiza, “Pa izi ine ndidzapemphanso:
zaka za dzanja lamanja la Wammwambamwamba.
11 Ine ndidzakumbukira ntchito za Yehova;
Ine ndidzakumbukira zodabwitsa zanu za kalekale.
12 Ndidzakumbukira ntchito zanu
ndi kulingalira zodabwitsa zanu.”
13 Njira zanu Mulungu ndi zoyera.
Kodi ndi mulungu uti ali wamkulu kuposa Mulungu wathu?
14 Inu ndinu Mulungu wochita zodabwitsa;
Mumaonetsera mphamvu yanu pakati pa mitundu ya anthu.
15 Ndi dzanja lanu lamphamvu munawombola anthu anu,
zidzukulu za Yakobo ndi Yosefe.
Sela
16 Madzi anakuonani Mulungu,
madzi anakuonani ndipo anachita mantha;
nyanja yozama inakomoka.
17 Mitambo inakhuthula madzi ake pansi,
mu mlengalenga munamveka mabingu;
mivi yanu inawuluka uku ndi uku.
18 Bingu lanu linamveka mʼmphepo ya kamvuluvulu,
mphenzi yanu inawalitsa dziko lonse;
dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.
19 Njira yanu inadutsa pa nyanja,
njira yanu inadutsa pa madzi amphamvu,
ngakhale zidindo za mapazi anu sizinaoneke.
20 Inu munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa
mwa dzanja la Mose ndi Aaroni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.