Masalimo 132
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
132 Inu Yehova, kumbukirani Davide
ndi mavuto onse anapirira.
2 Iye analumbira kwa Yehova
ndi kulonjeza kwa Wamphamvu wa Yakobo kuti,
3 “Sindidzalowa mʼnyumba mwanga
kapena kugona pa bedi langa:
4 sindidzalola kuti maso anga agone,
kapena zikope zanga ziwodzere,
5 mpaka nditamupezera malo Yehova,
malo okhala a Wamphamvu wa Yakobo.”
6 Zoonadi, tinamva za Bokosi la Chipangano ku Efurata,
tinalipeza mʼminda ya ku Yaara:
7 “Tiyeni tipite ku malo ake okhalamo;
tiyeni tikamulambire pa mapazi ake.
8 ‘Dzukani Yehova, ndipo bwerani ku malo anu opumulira,
Inuyo ndi Bokosi la Chipangano limene limafanizira mphamvu zanu.
9 Ansembe anu avekedwe chilungamo;
anthu anu oyera mtima ayimbe nyimbo mwachimwemwe.’ ”
10 Chifukwa cha Davide mtumiki wanu,
musakane wodzozedwa wanu.
11 Yehova analumbira kwa Davide,
lumbiro lotsimikizika kuti Iye sadzasintha:
“Mmodzi wa ana ako
ndidzamuyika pa mpando waufumu;
12 ngati ana ako azisunga pangano langa
ndi malamulo amene ndiwaphunzitsa,
pamenepo ana awo adzakhala pa mpando
wako waufumu kwamuyaya ndi muyaya.”
13 Pakuti Yehova wasankha Ziyoni,
Iye wakhumba kuti akhale malo ake okhalamo:
14 “Awa ndi malo anga opumapo ku nthawi za nthawi;
ndidzakhala pano pa mpando waufumu, pakuti ndakhumba zimenezi.
15 Ndidzadalitsa mzindawu ndi zinthu zambiri;
anthu ake osauka ndidzawakhutitsa ndi chakudya.
16 Ndidzaveka ansembe ake chipulumutso,
ndipo anthu ake oyera mtima adzayimba nthawi zonse nyimbo zachimwemwe.
17 “Pano ndidzachulukitsa mphamvu za Davide
ndi kuyikapo nyale ya wodzozedwa wanga.
18 Ndidzaveka adani ake manyazi,
koma chipewa chaufumu pamutu pake chidzakhala chowala.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.