Luka 10
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Yesu Atuma Ophunzira 72
10 Zitatha izi Ambuye anasankha enanso 72 ndi kuwatumiza awiriawiri patsogolo pake ku mzinda uliwonse ndi kumalo kumene Iye anatsala pangʼono kupitako. 2 Iye anawawuza kuti, “Zokolola ndi zambiri, koma ogwira ntchito ndi ochepa. Pemphani Ambuye wa zokolola, kuti atumize antchito ku munda wake wa zokolola. 3 Pitani! Ine ndikukutumizani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. 4 Musatenge chikwama kapena thumba kapena nsapato; ndipo musalonjere wina aliyense pa njira.
5 “Mukamalowa mʼnyumba, poyamba nenani kuti, ‘Mtendere pa nyumba ino.’ 6 Ngati mʼnyumbamo muli munthu wofuna mtendere, mtendere wanuwo udzakhala pa iyeyo; ngati mulibemo, mtendere wanuwo udzabwerera kwa inu. 7 Khalani mʼnyumba yomweyo, idyani ndi kumwa chilichonse chimene akupatsani, pakuti wantchito ayenera kulandira malipiro ake. Musachoke kumene mwafikirako ndi kupita ku nyumba zina.
8 “Mukamalowa mʼmudzi, ndi kulandiridwa, idyani chilichonse akukonzerani. 9 Chiritsani odwala amene ali kumeneko ndipo muwawuze kuti, ‘Ufumu wa Mulungu wayandikira.’ 10 Koma mukalowa mʼmudzi ndipo osalandiridwa bwino, kapiteni ku misewu mʼmudzimo nʼkukanena kuti, 11 ‘Tikukusansirani ngakhale fumbi la mʼmudzi wanuwu limene lamamatira ku mapazi athuwa. Komabe dziwani izi: Ufumu wa Mulungu wayandikira.’ 12 Ine ndikuwuzani kuti adzachita chifundo polanga Sodomu pa tsikulo kusiyana ndi mudziwo.
13 “Ndiwe watsoka, iwe Korazini! Ndiwe watsoka, iwe Betisaida! Kukanakhala kuti zodabwitsa zimene zinachitika mwa inu zinachitika ku Turo ndi Sidoni, iwo akanatembenuka mtima kale lomwe, atavala ziguduli ndi kudzola phulusa. 14 Koma adzachita chifundo polanga Turo ndi Sidoni kusiyana ndi inu. 15 Kodi iwe Kaperenawo, adzakukweza mpaka kumwamba? Ayi, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa.
16 “Womvera inu, akumvera Ine; wokana inu, akukana Ine. Ndipo wokana Ine; akukana Iye amene anandituma Ine.”
17 Anthu 72 aja anabwerera ndi chimwemwe ndipo anati, “Ambuye, ngakhale ziwanda zinatigonjera ife mʼdzina lanu.”
18 Iye anayankha kuti, “Ndinaona Satana akugwa kuchokera kumwamba ngati mphenzi. 19 Ine ndakupatsani ulamuliro woponda njoka ndi zinkhanira, ndi kugonjetsa mphamvu zonse za mdani; palibe chimene chidzakupwetekani. 20 Komabe musakondwere chifukwa mizimu yoyipa inakugonjerani, koma kondwerani chifukwa mayina anu analembedwa kumwamba.”
21 Nthawi imeneyo Mzimu Woyera anadzaza Yesu ndi chimwemwe ndipo anati, “Ine ndikulemekeza Inu, Atate Ambuye a kumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwawabisira anthu anzeru ndi ophunzira zinthu izi ndipo mwaziwulula kwa ana aangʼono. Inde, Atate, pakuti munachita zimenezi mwachifuniro chanu.
22 “Atate anga anapereka zinthu zonse mʼmanja mwanga. Palibe amene amadziwa Mwana kupatula Atate yekha, ndipo palibe amene amadziwa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuwululira.”
23 Kenaka anatembenukira kwa ophunzira ake nawawuza iwo okha kuti, “Ndi odala maso amene akuona zimene mukuonazi. 24 Pakuti kunena zoona aneneri ambiri ndi mafumu anafunitsitsa kuona zimene mukuonazi koma sanazione, ndi kumva zimene mukumvazi koma sanazimve.”
Fanizo la Msamariya Wachifundo
25 Nthawi ina katswiri wa malamulo anayimirira kuti ayese Yesu. Iye anati, “Aphunzitsi, ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?”
26 Yesu anayankha kuti, “Mwalembedwa chiyani mʼMalamulo, ndipo iwe umawerenga zotani?”
27 Iye anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini.”
28 Yesu anayankha kuti, “Iwe wayankha bwino, chita zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo.”
29 Koma iye anafuna kudzilungamitsa yekha, ndipo anamufunsanso Yesu kuti, “Kodi mnansi wanga ndani?”
30 Yesu pomuyankha anati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira anavulazidwa ndi achifwamba. Anamuvula zovala zake, namumenya ndi kuthawa, namusiya ali pafupi kufa. 31 Wansembe ankapita pa njira yomweyo, ndipo ataona munthuyo, analambalala. 32 Chimodzimodzinso, Mlevi wina pamene anafika pa malopo ndi kumuona, analambalalanso. 33 Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, anafika pamene panali munthuyo; ndipo atamuona, anamva naye chisoni. 34 Anapita panali munthu wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa zilonda zake, nʼkuzimanga. Kenaka anamukweza pa bulu wake, napita naye ku nyumba ya alendo, namusamalira. 35 Mmawa mwake anatenga ndalama ziwiri zasiliva nazipereka kwa woyangʼanira nyumbayo, nati, ‘Musamalireni munthuyu, ndipo pobwera ndidzakubwezerani zonse zimene mugwiritse ntchito.’
36 “Kodi ukuganiza ndi ndani mwa atatuwa, amene anali mnansi wa munthu amene anavulazidwa ndi achifwambawo?”
37 Katswiri wa Malamulo uja anayankha kuti, “Amene anamuchitira chifundo.”
Yesu anamuwuza kuti, “Pita, uzikachita chimodzimodzi.”
Marita ndi Mariya
38 Yesu ndi ophunzira ake akuyenda, anafika pa mudzi kumene mayi wotchedwa Marita anamulandira Iye mʼnyumba mwake. 39 Mayiyu anali ndi mchemwali wake wotchedwa Mariya, amene anakhala pa mapazi a Yesu kumverera zimene Iye ankanena. 40 Koma Marita anatanganidwa ndi zokonzekera zonse zimene zimayenera kuchitika. Iye anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Ambuye, kodi simusamala kuti mchemwali wanga wandisiya kuti ndichite ntchito yonse ndekha? Muwuzeni andithandize!”
41 Ambuye anati, “Marita, Marita, ukudandaula ndi kuvutika ndi zinthu zambiri, 42 koma chofunika nʼchimodzi chokha. Mariya wasankha chinthu chabwino, ndipo palibe angamulande chimenechi.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.