Levitiko 26
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mphotho ya Kumvera
26 “ ‘Musadzipangire mafano ndipo musayimike chifanizo chosema kapena mwala woti mudzipembedza. Musayike mwala wosema mʼdziko mwanu kuti muziwugwadira. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
2 “ ‘Muzisunga Masabata anga ndipo muzilemekeza malo anga wopatulika. Ine ndine Yehova.
3 “ ‘Mukamayenda motsata malangizo anga ndi kumvera mosamalitsa malamulo anga, 4 ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake. Nthaka yanu idzabala zokolola zake, ndipo mitengo ya mʼmunda idzabala zipatso zake. 5 Mudzakhala mukupuntha tirigu mpaka nthawi yothyola mphesa, ndipo mudzakhala mukuthyola mphesa mpaka nthawi yodzala. Mudzadya chakudya chanu mpaka kukhuta ndipo mudzakhala mʼdziko lanu mwamtendere.
6 “ ‘Ndidzabweretsa mtendere mʼdziko lanu, ndipo muzidzagona popanda wokuopsezani. Ndidzachotsa nyama zakuthengo zoopsa mʼdziko mwanu, ndipo mʼdzikomo simudzakhala nkhondo. 7 Mudzapirikitsa adani anu, ndipo mudzawagonjetsa ndi lupanga pamaso panu. 8 Anthu asanu mwa inu adzapirikitsa anthu 100, ndipo anthu 100 mwa inu adzathamangitsa anthu 10,000, ndipo adani anuwo mudzawagonjetsa ndi lupanga.
9 “ ‘Ndidzakukumbukirani ndi kukupatsani ana ambiri ndi kukuchulukitsani. Ndidzasunga pangano langa ndi inu. 10 Mudzakhala mukudyabe chakudya chogonera ndipo mudzachotse chakudyacho mʼnkhokwe kuti mupezemo malo woyika chakudya china chatsopano. 11 Ndidzakhala pakati panu, ndipo sindidzayipidwa nanu. 12 Ine ndidzayendayenda pakati panu ndipo ndidzakhala Mulungu wanu. Inu mudzakhala anthu anga. 13 Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti musakhalenso akapolo a Aigupto. Ndinadula mipiringidzo ya goli lanu ndi kukuthandizani kuti muziyenda momasuka.
Chilango Chakusamvera
14 “ ‘Koma mukadzapanda kundimvera ndi kuphwanya malamulo anga onsewa, 15 ndipo ngati mudzanyoza malangizo anga ndi kunyansidwa ndi malamulo anga, ndi kulephera kumvera zonse zimene ndakulamulani, ndi kuswa pangano langa, 16 Ine ndidzakuchitirani izi: ndidzabweretsa zoopsa zadzidzidzi monga chifuwa chachikulu chowondetsa ndiponso malungo amene adzawononga maso ndi kufowoketsa moyo wanu. Mudzangovutika kudzala mbewu zanu chifukwa adani anu adzazidya. 17 Ndidzakufulatirani, kotero kuti adani anu adzakugonjetsani. Odana nanu adzakulamulirani ndipo inu muzidzagothawa popanda wokupirikitsani.
18 “ ‘Ngati simudzandimvera mutaona zonsezi, ndidzakulanganinso mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu. 19 Ndidzathyola mphamvu zanu zimene mukunyadirazo, ndipo ndidzasandutsa mitambo kuti ikhale yowuma ngati chitsulo, ndiponso nthaka yanu kuti ikhale ngati mkuwa. 20 Mphamvu zanu zidzapita pachabe chifukwa nthaka yanu sidzabala kanthu, ngakhale mitengo yake sidzabala zipatso zake.
21 “ ‘Ngati mudzapitirira kutsutsana nane ndi kukana kundimvera, ndidzachulukitsa masautso anu kasanu ndi kawiri molingana ndi machimo anu. 22 Ndidzabweretsa zirombo zolusa pakati panu, ndipo zidzakulandani ana anu ndi kuwononga ngʼombe zanu. Choncho zidzachepetsa chiwerengero chanu kotero kuti mʼnjira mwanu simudzapita anthu.
23 “ ‘Mukadzapanda kutembenukira kwa Ine ngakhale nditakulangani motere, ndi kumachitabe zotsutsana ndi Ine, 24 Ine mwini ndidzalimbana nanu, ndipo ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha machimo anu. 25 Ndipo ndidzabweretsa lupanga pa inu ndi kukulangani chifukwa chophwanya pangano langa. Mukadzasonkhana mʼmizinda yanu, ndidzatumiza miliri pakati panu ndipo ndidzakuperekani mʼmanja mwa adani anu. 26 Ndikadzachepetsa buledi wanu, akazi khumi adzaphika buledi wawo mu uvuni umodzi, ndipo adzakugawirani bulediyo pangʼonopangʼono. Choncho mudzadya koma wosakhuta.
27 “ ‘Mukadzapanda kundimvera ngakhale nditakulangani motere, ndi kumatsutsanabe ndi Ine, 28 pamenepo ndidzalimbana nanu mwaukali, ndipo Ine mwini ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu. 29 Mudzadya ana anu aamuna ndiponso mudzadya ana anu aakazi. 30 Ine ndidzawononga malo anu opembedzera mafano a ku mapiri. Ndidzagwetsa maguwa anu ofukizira lubani, ndipo ndidzawunjika pamodzi mitembo ya mafano anu wopanda moyowo, ndipo ndidzanyansidwa nanu. 31 Ndidzasandutsa mizinda yanu kukhala mabwinja ndi kuwononga malo anu wopatulika. Sindidzakondweranso ndi fungo lokoma la zopereka zanu. 32 Ndidzawononga dziko kotero kuti adani anu mʼmenemo adzadabwa. 33 Ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndipo ndidzasolola lupanga langa ndi kukupirikitsani. Dziko lanu lidzawonongedwa, ndipo mizinda yanu idzasanduka mabwinja. 34 Nthawi imeneyo nthaka idzasangalalira kuyipumitsa kwake nthawi yonse imene idzakhala yosalimidwa, pamene inu mudzakhala muli mʼdziko la adani anu. Pa nthawi imeneyo dziko lidzapumula ndi kukondwerera kulipumuza kwake. 35 Nthawi zonse pamene dzikolo lidzakhala lopanda anthu, nthaka idzapumula. Mpumulo umenewu udzakhala umene nthakayo sinapumulepo pa nthawi zimene inu munkapumula muli mʼdzikomo.
36 “ ‘Kunena za amene adzatsale, ndidzayika mantha mʼmitima mwawo mʼdziko la adani awo kotero kuti adzathawa ngakhale mtswatswa wa tsamba lowuluka ndi mphepo. Adzathawa ngati akuthawa lupanga, ndipo adzagwa pansi ngakhale padzakhale wopanda kuwapirikitsa. 37 Iwo adzaphunthwitsana ngati akuthawa nkhondo, ngakhale padzakhale popanda wowapirikitsa. Choncho simudzatha kuyima pamaso pa adani anu. 38 Mudzatheratu pakati pa mitundu ya anthu. Dziko la adani anu lidzakudyani. 39 Ngakhale iwo amene adzatsale adzatheratu mʼdziko la adani awo chifukwa cha machimo awo ndi machimo a makolo awo.
40 “ ‘Tsono adzawulula machimo awo ndi machimo a makolo awo, kusakhulupirika kwawo ndi mayendedwe awo otsutsana nane, 41 zomwe zinandipangitsa kuwafulatira ndi kuwapereka mʼmanja mwa adani awo. Ndipo mitima yawo yowumayo ikadzadzichepetsa ndi kuvomera kulangidwa chifukwa cha machimo awo, 42 Ine ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo, pangano langa ndi Isake, pangano langa ndi Abrahamu. Ndidzakumbukiranso dzikolo. 43 Pakuti adzasiya dziko lawo lopanda anthu, nthaka idzakondwerera zaka zake zoyipumuza pamene iwo kudzakhala kulibe. Koma adzalangidwa chifukwa cha machimo awo popeza anakana malamulo anga ndipo mitima yawo inkayipidwa nawo malangizo anga. 44 Komabe ngakhale adzachite zonsezi ali mʼdziko la adani awo, Ine sindidzawakana kapena kuyipidwa nawo kwakuti nʼkuwawononga kwathunthu ndi kuthetsa pangano langa ndi iwo. Ine ndine Yehova Mulungu wawo. 45 Koma powachitira chifundo, ndidzakumbukira pangano langa ndi makolo awo amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto mitundu ina ikuona kuti Ine ndikhale Mulungu wawo. Ine ndine Yehova.’ ”
46 Amenewa ndi malamulo ndi malangizo amene Yehova anawayika pakati pa Iye mwini ndi Aisraeli pa Phiri la Sinai kudzera mwa Mose.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.