Levitiko 22
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
22 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Uza Aaroni ndi ana ake kuti azilemekeza zinthu zopatulika zimene Aisraeli azipereka kwa Ine, kuti asayipitse dzina langa loyera. Ine ndine Yehova.
3 “Uwawuze kuti ngati wina aliyense mwa zidzukulu zawo mʼmibado yonse imene ikubwera adzayandikira zinthu zopatulika zimene ana a Israeli apereka kwa Yehova, ali wodetsedwa, ameneyo achotsedwe pamaso pa Yehova. Ine ndine Yehova.
4 “Munthu aliyense mwa zidzukulu za Aaroni amene ali ndi khate kapena amatulutsa zoyipa mʼthupi mwake, asadye zinthu zopatulika mpaka atayeretsedwa. Wansembe angakhale wodetsedwa atakhudzana ndi chinthu chimene chadetsedwa ndi chinthu chakufa kapena kukhudza munthu amene wataya umuna, 5 kapena kukhudza chilichonse chokwawa chomwe chimadetsa munthu, kapena kukhudza munthu amene angamudetse, kapenanso kukhudza kanthu kena kalikonse kodetsedwa. 6 Tsono ngati wansembe angakhudze chilichonse mwa zimenezi ndiye kuti adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Asadye chopereka chilichonse chopatulika mpaka atasamba thupi lake lonse. 7 Munthuyo adzakhala woyeretsedwa pamene dzuwa lalowa, ndipo angathe kudya chopereka chopatulikacho popeza ndi chakudya chake. 8 Wansembe sayenera kudya chinthu chofa chokha kapena chojiwa ndi chirombo kuopa kuti angadzidetse ndi chakudyacho. Ine ndine Yehova.
9 “ ‘Choncho ansembe azisunga malamulo angawa kuti asapezeke wolakwa ndi kufa chifukwa chopeputsa malamulowa. Ine ndine Yehova, amene ndimawayeretsa.
10 “ ‘Aliyense amene si wabanja la wansembe, kaya ndi mlendo wa wansembe, kapena wantchito wake, asadye chopereka chopatulika. 11 Koma kapolo amene wagulidwa ndi ndalama kapena kubadwira mʼbanja la wansembe angathe kudya chakudya cha wansembeyo. 12 Mwana wamkazi wa wansembe amene wakwatiwa ndi munthu amene si wansembe, asadyeko nsembe zopatulikazo. 13 Koma mwana wamkazi wa wansembe amene ali wamasiye kapena wosudzulidwa, ndipo alibe mwana, komanso anabwerera ku nyumba ya abambo ake monga pa nthawi ya utsikana wake, angathe kudya chakudya cha abambo ake. Mlendo asadye chakudya chopatulika.
14 “ ‘Ngati munthu wina aliyense adya chopereka chopatulika mosadziwa, munthuyo amubwezere wansembe chinthu chopatulikacho ndipo awonjezerepo limodzi la magawo asanu a chinthucho. 15 Choncho ansembe asayipitse zopereka zopatulika za Aisraeli zimene apereka kwa Yehova 16 ndipo asachimwitse ndi kupalamulitsa Aisraeli powalola kudya zakudya zawo zopatulika. Ine ndine Yehova amene ndimawayeretsa.’ ”
Nsembe Zosavomerezeka
17 Yehova anawuza Mose kuti, 18 “Yankhula ndi Aaroni, ana ake pamodzi ndi Aisraeli onse, ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati wina aliyense wa inu, Mwisraeli kapena mlendo amene akukhala mu Israeli abwera ndi mphatso ya nsembe yopsereza kwa Yehova, kupereka chimene analumbira kapena kuti ikhale nsembe yaufulu, 19 ndiye kuti abwere ndi ngʼombe yayimuna, nkhosa yayimuna kapena mbuzi yayimuna. Izi zikhale zopanda chilema kuti zilandiridwe. 20 Musapereke nyama iliyonse yokhala ndi chilema chifukwa sidzalandiridwa mʼmalo mwanu. 21 Pamene wina aliyense abweretsa ngʼombe kapena nkhosa kuti ikhale nsembe yachiyanjano kwa Yehova, kukwaniritsa zimene analumbira kapena kuti ikhale nsembe yaufulu, nyamayo iyenera kukhala yangwiro ndi yopanda chilema kuti ilandiridwe. 22 Musapereke kwa Yehova nyama zakhungu, zovulala kapena zolumala, kapena nyama zimene zikutulutsa mafinya mʼthupi mwake, kapena zimene zili ndi nthenda yonyerenyetsa, kapena zimene zili ndi mphere. Nyama zotere musaziyike pa guwa kuti zikhale nsembe yopsereza kwa Yehova. 23 Koma mungathe kupereka ngʼombe yayimuna kapena nkhosa imene ili ndi chiwalo chachitali kapena chachifupi kukhala nsembe yaufulu. Koma simungayipereke ngati nsembe yoperekera zimene munalumbirira chifukwa sidzalandiridwa. 24 Nyama iliyonse imene mavalo ake ndi onyuka kapena ophwanyika, ongʼambika kapena oduka, musamayipereke kwa Yehova mʼdziko lanu. 25 Ndipo musalandire nyama zotere kuchokera kwa mlendo ndi kuzipereka kukhala zakudya za Mulungu wanu. Zimenezi sizidzalandiridwa mʼmalo mwanu chifukwa zili ndi chilema ndipo ndi zolumala.’ ”
26 Yehova anawuza Mose kuti, 27 “Pamene mwana wangʼombe, mwana wankhosa kapena mwana wambuzi wabadwa, akhale ndi make kwa masiku asanu ndi awiri. Kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu mpaka mʼtsogolo mwake, angathe kulandiridwa kuti akhale nsembe yopsereza ya kwa Yehova. 28 Musaphe ngʼombe kapena nkhosa pamodzi ndi mwana wake tsiku limodzi. Muyidye pa tsiku lomwelo; musasiyeko ina mpaka mmawa. Ine ndine Yehova.
29 “Pamene mupereka nsembe yoyamika kwa Yehova, muyipereke mwakufuna kwanu mu njira yoti ilandiridwe mʼmalo mwanu. 30 Muyidye pa tsiku lomwelo, wosasiyako ina mpaka mmawa. Ine ndine Yehova.
31 “Choncho sungani malamulo anga ndi kuwatsatira. Ine ndine Yehova. 32 Musanyoze dzina langa loyera. Koma lilemekezedwe pakati pa Aisraeli. Ine ndine Yehova amene ndimakuyeretsani 33 ndipo ndine amene ndinakutulutsani mu Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.