Levitiko 15
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Zonyansa Zotuluka Mʼthupi
15 Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, 2 “Yankhulani ndi Aisraeli ndipo muwawuze kuti, ‘Mwamuna aliyense akakhala ndi nthenda yotulutsa mafinya ku maliseche ake, zotulukazo ndi zonyansa ndithu. 3 Lamulo lokhudza kudziyipitsira ndi zotuluka ku maliseche a munthu nali: Malisechewo akamatulukabe mafinya, kaya aleka, munthuyo adzakhala wodetsedwa:
4 “ ‘Bedi lililonse limene munthu wotulutsa mafinyayo agonapo, ndiponso chinthu chilichonse chimene akhalepo chidzakhala chodetsedwa. 5 Aliyense wokhudza bedi la munthuyo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 6 Aliyense wokhala pa chinthu chimene munthu wotulutsa mafinyayo anakhalapo, achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
7 “ ‘Aliyense wokhudza thupi la munthu amene akutulutsa mafinyayo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
8 “ ‘Munthu wotulutsa mafinya akalavulira malovu munthu wina amene ndi woyeretsedwa, munthu ameneyo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
9 “ ‘Chilichonse chimene munthuyo akhalira akakwera pa kavalo chidzakhala chodetsedwa. 10 Ndipo aliyense wokhudza chimene anakhalira munthuyo adzakhala wodetsedwanso mpaka madzulo. Aliyense wonyamula chinthucho achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
11 “ ‘Munthu wotulutsa mafinyayo akakhudza munthu aliyense asanasambe mʼmanja, wokhudzidwayo achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
12 “ ‘Mʼphika wadothi umene munthu wotulutsa mafinyayo wakhudza awuphwanye, ndipo chiwiya chilichonse chamtengo achitsuke ndi madzi.
13 “ ‘Munthu wotulutsa mafinyayo akaona kuti wachira, awerenge masiku asanu ndi awiri akuyeretsedwa kwake kenaka achape zovala zake ndi kusamba pa kasupe, ndipo adzayeretsedwa. 14 Pa tsiku la chisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri kapena mawunda a nkhunda awiri ndi kubwera nazo pamaso pa Yehova pa khomo pa tenti ya msonkhano ndipo azipereke kwa wansembe. 15 Wansembe apereke zimenezo: imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera machimo a munthu wotulutsa mafinya uja pamaso pa Yehova.
16 “ ‘Mwamuna akataya pansi mbewu yake yaumuna, asambe thupi lake lonse. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 17 Chovala chilichonse kapena chikopa chilichonse pomwe pagwera mbewu yaumunayo achichape, komabe chidzakhala chodetsedwa mpaka madzulo. 18 Mwamuna akagona ndi mkazi wake nataya mbewu yake yaumuna, onse awiriwo asambe. Komabe adzakhala odetsedwa mpaka madzulo.
19 “ ‘Mkazi akakhala wosamba ndipo ikakhala kuti ndi nthawi yake yeniyeni yosamba, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri. Aliyense amene adzamukhudza adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
20 “ ‘Chilichonse chimene mkaziyo agonera pa nthawi yake yosamba chidzakhala chodetsedwa, ndipo chilichonse chimene adzakhalira chidzakhalanso chodetsedwa. 21 Aliyense wokhudza bedi lake achape zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 22 Aliyense wokhudza chimene wakhalapo achape zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 23 Kaya ndi bedi kapena chinthu china chilichonse chimene anakhalapo, ngati munthu wina akhudza chinthucho, munthuyo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
24 “ ‘Mwamuna aliyense akagona naye ndipo magazi osamba kwake ndi kumukhudza, munthuyo adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri, ndipo bedi limene wagonapo lidzakhalanso lodetsedwa.
25 “ ‘Mkazi akataya magazi masiku ambiri, wosakhala pa nthawi yake yosamba, kapena akamasambabe kupitirira nthawi yake yosamba, mkaziyo adzakhala wodetsedwa nthawi yonse imene akutaya magazi, monga momwe amakhalira pa masiku ake osamba. 26 Bedi lililonse limene mkaziyo adzagonapo pa masiku onse pamene ali wotaya magazi, ndiponso chilichonse chimene wakhalira chidzakhala chodetsedwa monga mmene chimakhalira chodetsedwa pa nthawi yake yosamba. 27 Aliyense amene adzakhudza zinthu zimenezo adzakhala wodetsedwa ndipo ayenera kuchapa zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
28 “ ‘Nthawi yosamba ikatha, mkaziyo awerenge masiku asanu ndi awiri, ndipo masikuwo akatha adzakhala woyeretsedwa. 29 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, mkaziyo atenge njiwa ziwiri kapena mawunda awiri, ndipo abwere nazo kwa wansembe pa khomo la Tenti ya Msonkhano. 30 Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera mkaziyo pamaso pa Yehova chifukwa cha matenda ake wosamba aja.
31 “ ‘Choncho muwayeretsa ana a Israeli nʼkudetsedwa kwawo kuti angafe pochita tchimo lowadetsa limene polichita limadetsa malo anga wokhalamo amene ali pakati pawo.’ ”
32 Amenewa ndi malamulo a munthu amene akutuluka mafinya kumaliseche kwake, komanso a munthu aliyense amene wadetsedwa ndi mbewu yaumuna, 33 mkazi wodwala chifukwa cha msambo komanso a mwamuna kapena mkazi amene akutulutsa mafinya kumaliseche kwake ndi mwamuna wogona ndi mkazi amene akusamba.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.