Hoseya 4
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Yehova Ayimba Mlandu Israeli
4 Inu Aisraeli, imvani mawu a Yehova,
chifukwa Yehova ali ndi mlandu ndi inu
amene mumakhala mʼdzikoli:
“Mʼdziko mwanu mulibe kukhulupirika, mulibe chikondi
mulibe kulabadira za Mulungu.
2 Muli kutemberera kokha, kunama ndi kupha.
Kuba ndi kuchita chigololo;
machimo achita kunyanya
ndipo akungokhalira kuphana.
3 Chifukwa chake dziko likulira
ndipo onse amene amakhalamo akuvutika;
zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga
ndiponso nsomba zamʼnyanja zikufa.
4 “Koma wina asapeze mnzake chifukwa,
wina aliyense asayimbe mlandu mnzake,
pakuti anthu ako ali ngati anthu
amene amayimba mlandu wansembe.
5 Mumapunthwa usana ndi usiku
ndipo aneneri amapunthwa nanu pamodzi.
Choncho ndidzawononga amayi anu.
6 Anthu anga akuwonongeka chifukwa chosadziwa.
“Pakuti mwakana kudziwa,
Inenso ndidzakukanani monga ansembe anga;
chifukwa mwayiwala lamulo la Mulungu wanu,
Inenso ndidzayiwala ana anu.
7 Ansembe ankati akachuluka
iwo ankandichimwiranso kwambiri;
iwo anasinthanitsa ulemerero wawo ndi chinthu china chonyansa.
8 Amalemererapo pa machimo a anthu anga
ndipo amafunitsitsa kuti anthuwo azipitiriza kuchimwa.
9 Ndipo zidzakhala motere: zochitikira anthu ena, zidzachitikiranso ansembe.
Ndidzawalanga onsewo chifukwa cha njira zawo,
ndidzawabwezera chifukwa cha machitidwe awo.
10 “Iwo azidzadya koma sadzakhuta;
azidzachita zachiwerewere koma sadzachulukana,
chifukwa anasiya Yehova
kuti adzipereke 11 ku zachiwerewere,
ku vinyo wakale ndi watsopano,
zimene zimachotsa nzeru zomvetsa zinthu
12 za anthu anga.
Anthu anga amapempha nzeru ku fano lamtengo
ndipo ndodo yawo yamtengo imawayankha.
Mzimu wachiwerewere umawasocheretsa;
iwo sakukhulupirika kwa Mulungu wawo.
13 Amapereka nsembe pamwamba pa mapiri
ndi kufukiza lubani pa zitunda,
pa tsinde pa mtengo wa thundu, mnjale ndi mkundi,
pamene pali mthunzi wabwino.
Nʼchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere
ndipo akazi a ana anu akuchita zigololo.
14 “Ine sindidzalanga ana anu aakazi
pamene iwo adzachita zachiwerewere,
kapena akazi a ana anu
pamene adzachita zigololo.
Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere,
ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi achiwerewere a ku malo opembedzerako.
Anthu amene alibe nzeru adzawonongeka ndithu!
15 “Ngakhale umachita chigololo, iwe Israeli,
Yuda asapezeke ndi mlandu wotere.
“Usapite ku Giligala.
Usapite ku Beti-Aveni.
Ndipo usalumbire kuti, ‘Pali Yehova wamoyo!’
16 Aisraeli ndi nkhutukumve,
ngosamva ngati ana angʼombe.
Kodi Yehova angathe kuwaweta bwanji
ngati ana ankhosa pa msipu wabwino?
17 Efereimu waphathana ndi mafano;
mulekeni!
18 Ngakhale pamene zakumwa zawo zatha,
amapitiriza kuchita zachiwerewere;
atsogoleri awo amakonda kwambiri njira zawo zochititsa manyazi.
19 Adzachotsedwa ndi kamvuluvulu
ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zawo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.