Hoseya 13
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Mkwiyo wa Yehova pa Israeli
13 Kale Efereimu ankati akayankhula, anthu ankanjenjemera;
anali wolemekezeka mu Israeli.
Koma analakwa popembedza Baala, motero anafa.
2 Tsopano akunka nachimwirachimwirabe;
akudzipangira mafano pogwiritsa ntchito siliva wawo,
zifanizo zopangidwa mwaluso,
zonsezo zopangidwa ndi amisiri.
Amanena za anthu awa kuti,
“Amatenga munthu ndi kumupereka nsembe
ndipo amapsompsona fano la mwana wangʼombe.”
3 Choncho adzakhala ngati nkhungu yammawa,
ngati mame amene amakamuka msanga,
ngati mungu wowuluka kuchokera pa malo opunthira tirigu,
ngati utsi umene ukutulukira pa zenera.
4 Koma Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
amene ndinakutulutsani mu Igupto.
Simuyenera kudziwa Mulungu wina, koma Ine ndekha,
palibe Mpulumutsi wina kupatula Ine.
5 Ndinakusamalira mʼchipululu,
mʼdziko lotentha kwambiri.
6 Pamene ndinawadyetsa, iwo anakhuta;
iwo atakhuta anayamba kunyada;
ndipo anandiyiwala Ine.
7 Motero ndidzawalumphira ngati mkango,
ndidzawabisalira mu msewu ngati kambuku.
8 Ngati chimbalangondo cholandidwa ana ake,
ndidzawambwandira ndi kuwathyolathyola.
Ndidzawapwepweta ngati mkango;
chirombo chakuthengo chidzawakhadzula.
9 “Iwe Israeli, wawonongedwa,
chifukwa ukutsutsana ndi Ine, ukutsutsana ndi mthandizi wako.
10 Kodi mfumu yako ili kuti, kuti ikupulumutse?
Olamulira ako a mʼmizinda yonse ali kuti,
amene iwe unanena za iwo kuti,
‘Patseni mfumu ndi akalonga?’
11 Choncho Ine ndinakupatsani mfumu mwachipseramtima,
ndipo ndinayichotsa mwaukali.
12 Kulakwa kwa Efereimu kwasungidwa,
machimo ake alembedwa mʼbuku.
13 Zowawa zonga za mayi pa nthawi yobala mwana zamugwera,
koma iye ndi mwana wopanda nzeru,
pamene nthawi yake yobadwa yafika
iyeyo safuna kutuluka mʼmimba mwa amayi ake.
14 “Ndidzawapulumutsa ku mphamvu ya manda;
ndidzawawombola ku imfa.
Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti?
Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti?
“Sindidzachitanso chifundo,
15 ngakhale Efereimu akondwe pakati pa abale ake,
mphepo ya kummawa yochokera kwa Yehova idzabwera,
ikuwomba kuchokera ku chipululu.
Kasupe wake adzaphwa
ndipo chitsime chake chidzawuma.
Chuma chake chonse chamtengowapatali
chidzafunkhidwa ndipo chidzatengedwa.
16 Anthu a ku Samariya adzalangidwa chifukwa cha zolakwa zawo,
chifukwa anawukira Mulungu wawo.
Adzaphedwa ndi lupanga;
ana awo adzaphedwa mowamenyetsa pansi,
akazi awo oyembekezera adzatumbulidwa pa mimba.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.