Hoseya 10
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
10 Israeli anali mpesa wotambalala;
anabereka zipatso zambiri.
Pamene zipatso zawo zinanka zichuluka,
anawonjezera kumanga maguwa ansembe.
Pamene dziko lake linkatukuka,
anakongoletsa miyala yake yopatulika.
2 Mtima wawo ndi wonyenga
ndipo tsopano ayenera kulangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo.
Yehova adzagumula maguwa awo ansembe
ndi kuwononga miyala yawo yopatulika.
3 Pamenepo anthuwo adzanena kuti, “Ife tilibe mfumu
chifukwa sitinaope Yehova.
Koma ngakhale tikanakhala ndi mfumu,
kodi mfumuyo ikanatichitira chiyani?”
4 Mafumu amalonjeza zambiri,
amalumbira zabodza
pochita mapangano.
Kotero maweruzo amaphuka
ngati zitsamba zakupha mʼmunda umene walimidwa.
5 Anthu amene amakhala mu Samariya akuchita mantha
chifukwa cha fano la mwana wangʼombe ku Beti-Aveni.
Anthu ake adzalirira fanolo,
chimodzimodzinso ansembe ake adamawo,
amene anakondwera ndi kukongola kwake,
chifukwa lachotsedwa pakati pawo ndi kupita ku ukapolo.
6 Fanolo lidzatengedwa kupita ku Asiriya
ngati mphatso kwa mfumu yayikulu.
Efereimu adzachititsidwa manyazi
chifukwa cha mafano ake amitengo.
7 Samariya ndi mfumu yake adzatengedwa kupita kutali
ngati kanthambi koyenda pa madzi.
8 Malo opembedzerako mafano a ku Aveni adzawonongedwa.
Ili ndiye tchimo la Israeli.
Minga ndi mitungwi zidzamera
ndi kuphimba maguwa awo ansembe.
Kenaka anthu adzawuza mapiri kuti, “Tiphimbeni!”
ndipo adzawuza zitunda kuti, “Tigwereni!”
9 “Iwe Israeli, wachimwa kuyambira mʼmasiku a Gibeya,
ndipo wakhala uli pomwepo.
Kodi nkhondo sinagonjetse anthu
ochita zoyipa ku Gibeya?
10 Pamene ndifunire, ndidzalanga anthuwo;
mitundu ya anthu idzasonkhanitsidwa kudzalimbana nawo,
kuwayika mʼndende chifukwa cha uchimo wawo waukulu.
11 Efereimu ndi mwana wangʼombe wamkazi wophunzitsidwa
amene amakonda kupuntha tirigu,
choncho Ine ndidzayika goli
mʼkhosi lake lokongolalo.
Ndidzasenzetsa Efereimu goli,
Yuda ayenera kulima,
ndipo Yakobo ayenera kutipula.
12 Mufese nokha chilungamo
ndipo mudzakolola chipatso cha chikondi changa chosasinthika.
Ndipo tipulani munda wanu wosalimidwawo;
pakuti ino ndi nthawi yofunafuna Yehova,
mpaka Iye atabwera
kudzakugwetserani mivumbi ya chilungamo.
13 Koma inu munadzala zolakwa,
mwakolola zoyipa;
mwadya chipatso cha chinyengo.
Chifukwa mumadalira mphamvu zanu
ndiponso ankhondo anu ochulukawo,
14 phokoso lankhondo lidzamveka pakati pa anthu anga
kotero kuti malinga anu onse adzawonongeka,
monga momwe Salimani anawonongera Beti-Aribeli pa nthawi ya nkhondo;
pamene anapha amayi pamodzi ndi ana awo omwe.
15 Momwemonso zidzakuchitikira, iwe Beteli
chifukwa kuyipa kwako ndi kwakukulu.
Tsiku limeneli likadzafika,
mfumu ya Israeli idzawonongedwa kwathunthu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.