Genesis 3
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Kuchimwa kwa Munthu
3 Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ”
2 Mkaziyo anati kwa njokayo, “Tikhoza kudya zipatso za mʼmitengo ya mʼmundawu, 3 koma Mulungu anati, ‘Musadye zipatso za mu mtengo umene uli pakati pa munda, ndipo musadzawukhudze kuti mungadzafe.’ ”
4 “Ndithudi simudzafa,” inatero njokayo kwa mkaziyo. 5 “Pakuti Mulungu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye zipatso za mu mtengowo, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wodziwa zabwino ndi zoyipa.”
6 Pamene mkaziyo anaona kuti mtengowo unali wabwino kudya ndi wokongola ndi kuti unali wopatsa nzeru, anatengako zipatso zake nadya. Zina anamupatsako mwamuna wake amene anali naye pomwepo ndipo naye anadyanso. 7 Kenaka maso awo anatsekuka, ndipo anazindikira kuti anali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nadzipangira zovala.
8 Kenaka munthu uja ndi mkazi wake anamva mtswatswa wa Yehova Mulungu akuyendayenda mʼmundamo madzulo a tsikulo, ndipo iwo anabisala pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya mʼmundamo. 9 Yehova Mulungu anayitana munthu uja kuti, “Uli kuti?”
10 Iye anayankha, “Ndinakumvani mʼmundamo, ndipo ndimaopa chifukwa ndinali maliseche; choncho ndinabisala.”
11 Ndipo anamufunsa, “Ndani anakuwuza kuti uli maliseche? Kodi wadya zipatso za mtengo umene ndinakulamulira kuti usadye?”
12 Koma munthu uja anati, “Mkazi amene munandipatsa kuti ndizikhala nayeyu anandipatsako chipatso cha mtengowo ndipo ndinadya.”
13 Tsono Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, “Wachitachi nʼchiyani?”
Mkaziyo anati, “Njoka inandinamiza, ndipo ndinadya.”
14 Choncho Yehova Mulungu anati kwa njokayo, “Popeza wachita zimenezi,
“Ndiwe wotembereredwa kuposa ziweto zonse
ndi nyama zakuthengo zonse.
Udzayenda chafufumimba
ndipo udzadya fumbi
masiku onse a moyo wako.
15 Ndipo ndidzayika chidani
pakati pa iwe ndi mkaziyo,
pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake;
Iye adzaphwanya mutu wako
ndipo iwe udzaluma chidendene chake.”
16 Kwa mkaziyo Iye anati,
“Ndidzachulukitsa ululu wako kwambiri pamene uli ndi pakati;
ndipo udzamva ululu pa nthawi yako yobereka ana.
Udzakhumba mwamuna wako,
ndipo adzakulamulira.”
17 Ndipo kwa Adamu Mulungu anati, “Chifukwa wamvera mkazi wako ndipo wadya zipatso za mu mtengo umene ndinakulamulira kuti, ‘Usadye.’
“Nthaka yatembereredwa chifukwa cha iwe,
movutikira udzadya zochokera mʼnthakamo
masiku onse a moyo wako.
18 Mʼnthakamo mudzamera minga ndi nthula
ndipo udzadya zomera zakuthengo.
19 Kuti upeze chakudya udzayenera
kukhetsa thukuta,
mpaka utabwerera ku nthaka
pakuti unachokera kumeneko;
pakuti ndiwe fumbi
ku fumbi komweko udzabwerera.”
20 Munthu uja anatcha mkazi wake Hava, chifukwa iyeyu adzakhala mayi wa anthu onse amoyo.
21 Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi mkazi wake zovala zachikopa ndipo anawaveka. 22 Ndipo Yehova Mulungu anati, “Tsopano munthu uyu wasanduka mmodzi wa ife, wodziwa zabwino ndi zoyipa. Iyeyu asaloledwe kutambasula dzanja ndi kutengako zipatso za mu mtengo wopatsa moyo uja kuti angakhale ndi moyo mpaka muyaya.” 23 Kotero Yehova Mulungu anatulutsa Adamu Mʼmunda wa Edeni kuti azilima mʼnthaka imene anachokera. 24 Atamuthamangitsa munthu uja, Yehova anayika Akerubi mbali ya kummawa kwa Munda wa Edeni ndi lupanga lamoto limene limayendayenda ponsepo, kuteteza njira ya ku mtengo wopatsa moyo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.