Ezekieli 23
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Za Yerusalemu ndi Samariya
23 Yehova anandiyankhula nati: 2 “Iwe mwana wa munthu, panali atsikana awiri ana a mayi mmodzi. 3 Iwo ankachita za chiwerewere ku Igupto. Za chiwerewerezo anayamba ali achichepere. Kumeneko anthu ankangowasisita pa chifuwa ndi kuwagwiragwira mawere awo aja. 4 Wamkulu dzina lake anali Ohola, ndipo mngʼono wakeyo anali Oholiba. Ine ndinawakwatira ndipo anabereka ana aamuna ndi ana aakazi. Ohola ndiye Samariya, ndipo Yerusalemu ndiye Oholiba.
5 “Ohola anachita zachiwerewere ngakhale anali mkazi wanga; ndipo iye anakangamira abwenzi ake a ku Asiriya. 6 Amenewo anali asilikali ovala zibakuwa zamlangali, abwanamkubwa ndiponso atsogoleri a nkhondo. Onsewo anali anyamata osiririka ndipo ankakwera pa akavalo. 7 Ohola anachita zachiwerewere ndi onsewa, anthu otchuka a ku Asiriya. Iye anadziyipitsa ndi mafano a munthu aliyense amene anagona naye. 8 Iye sanaleke za chiwerewere zimene anaziphunzira ku Igupto. Paja akanali mtsikana anyamata ankagona naye. Iwo ankamusisita mawere akanali anthete nachita naye zachiwerewere.
9 “Nʼchifukwa chake Ine ndinamupereka kwa achikondi ake, Asiriya, amene iye ankawalakalaka. 10 Iwowa anamuvula, namulanda ana ake aamuna ndi aakazi ndipo anamupha ndi lupanga. Ndipo atalangidwa choncho, iye anasanduka chinthu chonyozeka pakati pa akazi.
11 “Mphwake Oholiba anaona zimenezi natengerako. Koma iye anachita zachiwerewere kuposa mkulu wake. 12 Iyenso anakangamira Asiriya, abwanamkubwa, olamulira asilikali, ankhondo ovala zovala zonse za nkhondo ndi okwera pa akavalo. Onsewa anali anyamata osiririka. 13 Ndinaona kuti iyenso anadziyipitsa; ndipo onse awiriwo anatsata njira imodzi.
14 “Koma Oholiba uja anachita chigololo kopitirira mkulu wake. Iye anaona zithunzi za amuna pa khoma, zithunzi za Ababuloni zolembedwa ndi inki yofiira, 15 atamanga malamba mʼchiwuno mwawo ndi kuvala nduwira pa mitu yawo. Onse amaoneka ngati atsogoleri a magaleta a Ababuloni, mbadwa za ku Kaldeya. 16 Oholiba atangowaona, anawalakalaka ndipo anatuma amithenga ku Kaldeya kukawayitana. 17 Ndipo Ababuloni anabwera nʼkudzagona naye. Choncho mwa chilakolako chawo anamuyipitsa. Koma atamuyipitsa choncho, iye ananyansidwa nawo. 18 Iye atachita chiwerewere chake poyera ndi kuonetsa umaliseche wake, Ine ndinamuchokera monyansidwa monga mmene ndinachitira ndi mʼbale wake. 19 Koma anachitabe zachiwerewere osalekeza. Ankakumbukira masiku a ubwana wake pamene ankachita za chiwerewere mʼdziko la Igupto. 20 Kumeneko iye ankalakalaka zibwenzi zake, amene ziwalo zawo zinali ngati za abulu ndipo kutentha kwawo kunali ngati kwa akavalo. 21 Motero, iwe Oholiba unafuna kuchitanso zadama monga unkachitira ku Igupto pamene unali mtsikana. Nthawi imene ija ankakusisita pa chifuwa ndi kugwiragwira mawere ako osagwa aja.
22 “Tsono iwe Oholiba, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakudzutsira zibwenzi zako zimene unkanyansidwa nazo zija kuti zilimbane nawe. Ndidzaziyitana kuti zibwere kuchokera mbali zonse. 23 Ndidzayitana anthu a ku Babuloni ndi Akaldeya onse, anthu a ku Pekodi, Sowa ndi Kowa pamodzi ndi Asiriya onse. Onsewa ndi amuna osiririka, abwanamkubwa, atsogoleri a ankhondo, oyenda pa magaleta, anthu a maudindo akuluakulu. Onsewa ndi okwera akavalo. 24 Iwo adzabwera kudzalimbana nawe ndi zida za nkhondo, magaleta ndi ngolo, pamodzi ndi anthu ambiri. Adzakuzinga mbali zonse atavala zishango zankhondo ndi zipewa zankhondo. Ndidzakupereka kwa iwo kuti akulange ndipo adzakulanga monga momwe adzafunire. 25 Ndidzaonetsa mkwiyo wanga pa iwe ndipo iwo adzakulanga iwe mwankhanza. Adzadula mphuno zanu ndi makutu anu, ndipo amene adzatsalira mwa iwe adzaphedwa ndi lupanga. Iwo adzakulanda ana ako aamuna ndi aakazi ndipo amene adzatsalira adzaphedwa ndi moto. 26 Adzakuvulaninso zovala zanu ndikukulandani zodzikongoletsera zanu zamtengowapatali. 27 Motero ndidzathetsa zonyansa zako ndi zachigololo zomwe unaziyamba ku Igupto. Choncho sudzalakalaka za ku Igupto kapena kuzikumbukiranso.
28 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndikukupereka mʼmanja mwa amene amadana nawe, kwa iwo amene unawafulatira moyipidwa nawo. 29 Adzachita nawe mwachidani. Adzakulanda zonse zimene unagwirira ntchito. Adzakusiya wamaliseche ndiponso wausiwa. Kuyipa kwa makhalidwe ako achiwerewere kudzakhala pammbalambanda. Zonyansa zako ndi chiwerewere chako, 30 zabweretsa izi pa iwe chifukwa unachita zonyansa ndi anthu a mitundu ndi kudziyipitsa ndi mafano awo. 31 Unatsata zochita za mkulu wako; choncho Ine ndidzayika chikho cha chilango chake mʼdzanja lako.
32 “Ine Ambuye Yehova ndikuti:
“Udzamwera chikho cha mkulu wako,
chikho chachikulu ndi chakuya;
anthu adzakuseka ndi kukunyoza,
pakuti chikhocho ndi chodzaza kwambiri.
33 Udzaledzera ndipo mtima wako udzadzaza ndi chisoni.
Chimenechi ndi chikho chachiwonongeko ndi chipasupasu,
chikho cha mkulu wako Samariya.
34 Udzamwa chikhocho mpaka kugugudiza.
Tsono udzaphwanyaphwanya chikhocho
ndipo udzangʼamba mawere ako ndi zigoba zake.
Ine ndayankhula, akutero Ambuye Yehova.
35 “Chifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza wandiyiwala Ine ndi kundifulatira, chomwecho uyenera kulangidwa chifukwa cha zonyansa zako ndi chiwerewere chako.”
36 Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi udzaweruza Ohola ndi Oholiba? Tsono uwayimbe mlandu chifukwa cha machitidwe awo onyansa. 37 Iwo achita chigololo ndipo anapha anthu. Anachita chigololo popembedza mafano awo. Ngakhale ana amene anandiberekera Ine anawapereka kwa mafanowo ngati chakudya chawo. 38 Anachitanso izi: Iwo anayipitsa malo anga opatulika ndi kudetsa masabata anga. 39 Atapereka ana awo kwa mafano, tsiku lomwelo anakalowanso mʼNyumba yanga yopatulika ndi kuyipitsamo. Izi ndi zimene anachita mʼNyumba mwanga.
40 “Iwo anatuma amithenga kukayitana amuna a ku mayiko akutali. Anthuwo atabwera, abale awiri aja anasambasamba, kudzola utoto wodzikometsera kumaso, kenaka ndi kuvala zovala zamakaka. 41 Anakhala pa bedi lokongola ndipo patsogolo pawo panali tebulo pamene munayikapo lubani ndi mafuta. Zonse zowapatsa Ine.
42 “Mfuwu wa chigulu cha anthu unamveka. Anthu oledzera ochokera ku chipululu anabwera pamodzi ndi anthu wamba ndipo anaveka akaziwo zibangiri kumanja ndi zipewa zaufumu zokongola ku mutu. 43 Ndipo ine ndinati za mkazi wotheratu ndi chigololoyo, ‘Tsono asiyeni kuti achite naye monga wachiwerewere, pakuti ichi ndi chimene iye ali basi.’ 44 Tsono anapita kwa iwo monga mmene anthu amapitira kwa mkazi wadama. Momwemo anapita kwa Ohola ndi kwa Oholiba kukachita nawo zadama. 45 Koma anthu olungama adzawazenga anthuwa mlandu wa chigololo ndi wa kupha anthu. Ndi iwodi anthu achigololo ndiponso mʼmanja mwawo muli magazi.
46 “Ambuye Yehova akuti: Itanitsani chigulu cha anthu kuti chidzawalange ndi kulanda chuma chawo. 47 Anthuwo adzawaponye miyala akazi awiriwo ndi kuwatema ndi malupanga awo. Ana awo aamuna ndi aakazi adzawaphe ndi kutentha nyumba zawo.
48 “Motero Ine ndidzathetsa zachigololo mʼdzikomo, ndipo akazi onse adzatengapo phunziro kuti asadzachite zachigololo monga za iwowo. 49 Ndidzawalanga chifukwa cha ntchito zawo za dama ndipo adzazunzika chifukwa cha tchimo lawo lopembedza mafano. Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.