Eksodo 25
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Zopereka Zomangira Chihema
25 Yehova ananena kwa Mose kuti, 2 “Uza Aisraeli kuti abweretse chopereka kwa Ine. Iwe ulandire choperekacho mʼmalo mwanga kuchokera kwa munthu amene akupereka mwakufuna kwake. 3 Zopereka zimene ulandire kwa anthuwo ndi izi: Golide, siliva ndi mkuwa. 4 Nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa, ubweya wambuzi; 5 zikopa za nkhosa zazimuna za utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu; matabwa amtengo wa mkesha; 6 mafuta anyale a olivi, zonunkhiritsa mafuta odzozera ndi zopangira lubani wonunkhira; 7 miyala yokongola ya mtundu wa onikisi ndi ina yabwino yoyika pa efodi ndi pa chovala cha pachifuwa.
8 “Iwo andipangire malo wopatulika, ndipo Ine ndidzakhala pakati pawo. 9 Umange chihema ndiponso ziwiya zamʼkatimo monga momwe Ine ndidzakuonetsere.
Bokosi la Chipangano
10 “Tsono apange bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha, ndipo kutalika kwake kukhale masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. 11 Bokosilo ulikute ndi golide wabwino kwambiri, mʼkati mwake ndi kunja komwe, ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira bokosilo. 12 Upange mphete zinayi zagolide ndipo uzimangirire ku miyendo yake inayi ya bokosilo, mbali ina ziwiri ndi mbali inanso ziwiri. 13 Kenaka upange mizati yamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide. 14 Ndipo ulowetse nsichizo mʼmphete zija za mbali zonse ziwiri za bokosilo kuti azinyamulira. 15 Nsichizo zizikhala mʼmphete za bokosilo nthawi zonse, zisamachotsedwe. 16 Ndipo udzayike mʼbokosilo miyala iwiri yolembedwapo malamulo imene Ine ndidzakupatse.
17 “Upange chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69. 18 Ndipo upange Akerubi awiri agolide osula ndi nyundo, uwayike mbali ziwiri za chivundikirocho, 19 kerubi mmodzi mbali ina ndi wina mbali inayo. Akerubiwa uwapangire limodzi ndi chivundikirocho mʼmapeto mwa mbali ziwirizo. 20 Mapiko a Akerubiwo adzatambasukire pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo kuti achiphimbe. Akerubiwo adzakhale choyangʼanana, aliyense kuyangʼana chivundikirocho. 21 Uyike chivundikirocho pamwamba pa bokosi ndipo mʼbokosilo uyikemo miyala ya malamulo, imene ndidzakupatse. 22 Ndizidzakumana nawe pamenepo, pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo, pakati pa Akerubi awiriwo, ndikumadzakupatsa malamulo onse okhudzana ndi Aisraeli.
Tebulo la Buledi Woperekedwa kwa Mulungu
23 “Upange tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69. 24 Tebulolo ulikute ndi golide wabwino kwambiri ndipo upange mkombero wagolide mʼmbali mwake. 25 Upange feremu yozungulira tebulo, mulifupi mwake ngati chikhatho cha dzanja, ndipo uyike mkombero wagolide kuzungulira feremuyo. 26 Upange mphete zinayi zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya zake zinayi, kumene kuli miyendo yake inayi. 27 Mphetezo uziyike kufupi ndi feremu kuti azikolowekamo nsichi zonyamulira tebuloyo. 28 Upange nsichi zamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide kuti azinyamulira tebulolo. 29 Upange mbale ndi zipande zagolide wabwino, pamodzinso ndi mitsuko ndi mabeseni zogwiritsa ntchito popereka nsembe. 30 Pa tebulopo uyikepo buledi woperekedwa kosalekeza, kuti azikhala pamaso panga nthawi zonse.
Choyikapo Nyale
31 “Upange choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zikhale zosulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zipangidwire kumodzi. 32 Mʼmbali mwake mukhale mphanda zisanu ndi imodzi, zitatu mbali iliyonse. 33 Zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa zikhale pa mphanda yoyamba. Pa mphanda yachiwiri pakhalenso zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa. Ndipo mphanda zonse zisanu ndi imodzi zikhale chimodzimodzi ndipo zituluke mʼchoyikapo nyalecho. 34 Pa choyikapo nyalecho pakhale zikho zinayi zopangidwa ngati maluwa amtowo ali ndi mphukira ndi maluwa. 35 Mphukira yoyamba ikhale mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zoyamba za pa choyikapo nyale. Mphukira yachiwiri ikhale mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zinazo. Ndipo mphukira yachitatu ikhale mʼmunsi mwa nthambi zina ziwirinso. Zonse pamodzi zikhale nthambi zisanu ndi imodzi 36 Mphukira ndi nthambi zonse zisulidwe kumodzi ndi choyikapo nyalecho ndi golide wabwino kwambiri.
37 “Ndipo upange nyale zisanu ndi ziwiri ndi kuziyika pa choyikapo nyalecho kuti ziwunikire kutsogolo. 38 Mbaniro ndi zowolera phulusa zikhale zagolide wabwino kwambiri. 39 Choyikapo nyale ndi zipangizo zonse zipangidwe ndi golide wabwino kwambiri wolemera makilogalamu 34. 40 Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.