Eksodo 18
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Yetero Abwera Kudzaona Mose
18 Yetero wansembe wa ku Midiyani amenenso anali mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu anachitira Mose ndi anthu ake a Aisraeli ndi mmene Yehova anawatulutsira mʼdziko la Igupto.
2 Mose atamubweza Zipora, mkazi wake, Yetero, mpongozi wake anamulandira 3 mwana wake wamkaziyo pamodzi ndi ana ake aamuna awiri. Mose anamupatsa mwana wachisamba dzina loti Geresomu popeza anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko lachilendo.” 4 Ndipo mwana wake wachiwiri anamupatsa dzina loti Eliezara, pakuti anati, “Mulungu wa makolo anga anali thandizo langa. Iye anandipulumutsa ku lupanga la Farao.”
5 Yetero, mpongozi wa Mose pamodzi ndi ana a Mose aamuna awiri ndi mkazi wake anabwera kwa Mose ku chipululu pa phiri la Mulungu kumene Mose anamanga misasa. 6 Yetero anali atatumiza uthenga kwa Mose kuti, “Ine Yetero, mpongozi wako, ndikubwera ndi mkazi wako ndi ana ake awiri.”
7 Kotero Mose anatuluka kukakumana ndi mpongozi wake ndipo anawerama ndi kupsompsona. Atalonjerana anakalowa mu tenti 8 Mose anafotokozera mpongozi wake zonse zimene Yehova anamuchita Farao ndi Aigupto chifukwa cha Israeli komanso zowawa zonse anakumana nazo mʼnjira. Mose anafotokozanso momwe Yehova anawapulumutsira.
9 Yetero anakondwa kwambiri atamva zabwino zonse zimene Yehova anachitira Aisraeli powapulumutsa mʼdzanja la Aigupto. 10 Iye anati, “Alemekezeke Yehova amene wakupulumutsani mʼdzanja la Aigupto ndi Farao. Wapulumutsanso anthuwa mʼdzanja la Aigupto. 11 Tsopano ndikudziwa kuti Yehova ndi wopambana milungu ina yonse, pakuti anachita izi kwa amene ananyoza Israeli.” 12 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Mulungu. Aaroni ndi akuluakulu onse a Israeli anabwera kudzadya chakudya pamodzi ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.
13 Mmawa mwake, Mose anakhala pa mpando kuti aweruze milandu ya anthu. Anthu anayima momuzungulira kuyambira mmawa mpaka madzulo. 14 Mpongozi wa Mose ataona zonse zimene iye amawachitira anthu anati, “Nʼchiyani chimene mukuwachitira anthuwa? Nʼchifukwa chiyani mulipo nokha woweruza, pamene anthu onsewa ayimirira kuyambira mmawa mpaka madzulo?”
15 Mose anamuyankha kuti, “Chifukwa anthuwa anabwera kwa ine kudzafunsa zimene Mulungu akufuna. 16 Ngati munthu akangana ndi mʼbale wake, onse awiri amabwera kwa ine, ndipo ine ndimawaweruza. Ndimawawuzanso malamulo a Mulungu ndi malangizo ake.”
17 Mpongozi wa Mose anayankha kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwino. 18 Ntchitoyi ndi yayikulu kuposa mphamvu zanu. Inu simungathe kuyigwira nokha. Inu pamodzi ndi anthuwa amene amabwera kwa inu mudzatopa. 19 Tsono tamverani ndikulangizeni, ndipo Mulungu akhale nanu. Inu muziwayimirira anthuwa pamaso pa Mulungu, ndipo mikangano yawo muzibwera nayo kwa Iye. 20 Aphunzitseni mawu ndi malangizo a Mulungu. Aphunzitseni mmene ayenera kukhalira ndi zimene ayenera kuchita. 21 Koma sankhani amuna odziwa ntchito yawo, anthu owopa Mulungu, anthu odalirika amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo. Tsono muwayike kuti akhale oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50 ndi ena a anthu khumi. 22 Tsono amenewa aziweruza anthu nthawi zonse. Mlandu uliwonse waukulu azibwera nawo kwa inu, koma mlandu waungʼono aziweruza okha. Izi zidzachititsa kuti ntchito yanu ipepuke, popeza mudzagwira ntchito mothandizana. 23 Ngati mutsatira malangizowa monga mmene Mulungu wakulamulirani ndiye kuti simudzafowoka ndipo anthu onsewa adzapita kwawo mu mtendere.”
24 Mose anamvera mpongozi wake ndi kuchita zonse zimene iye ananena. 25 Iye anasankha amuna odziwa bwino ntchito zawo ndipo anawayika kuti akhale atsogoleri, oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 500, ena a anthu makumi asanu ndi ena a anthu khumi. 26 Iwowa ankaweruza anthu nthawi zonse. Milandu yovuta ankabwera nayo kwa Mose, koma yosavuta ankayiweruza okha.
27 Kenaka Mose analola kuti mpongozi wake, Yetero anyamuke kubwerera ku dziko la kwawo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.