Deuteronomo 6
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Konda Yehova Mulungu Wako
6 Awa ndi malamulo, malangizo ndi ziphunzitso zimene Yehova Mulungu wanu anandilamula kuti ndikuphunzitseni kuti mukawatsatire mʼdziko limene mukuwolokera Yorodani kuti mukalitenge, 2 kuti inuyo, ana anu, ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo mudzaope Yehova Mulungu wanu moyo wanu wonse posunga malangizo ndi malamulo ake onse amene ndinakupatsani inu kuti musangalale ndi moyo wautali. 3 Mvera Israeli ndipo usamalitse kuchita malamulowa kuti zinthu zikuyendere bwino mʼdziko ndi kuti muchuluke kwambiri mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani.
4 Tamvani inu Aisraeli, Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi. 5 Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse. 6 Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. 7 Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka. 8 Muwamange ngati zizindikiro pa manja anu ndi kuwamangirira pa zipumi zanu. 9 Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu.
10 Pamene Yehova Mulungu wanu akukulowetsani ndi kukupatsani dziko limene analumbirira makolo anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo, dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu imene inu simunamange, 11 nyumba zodzaza ndi zinthu za mitundu yonse zimene inu simunayikemo, zitsime zimene inu simunakumbe, minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi zimene inuyo simunadzale, tsono mukadya ndi kukhuta, 12 samalani kuti mungayiwale Yehova amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani mu ukapolo.
13 Muziopa Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iye yekha, ndipo muzilumbira pa dzina lake. 14 Musamatsatire milungu ina, milungu ya anthu ena okuzungulirani, 15 pakuti Yehova Mulungu wanu amene ali pakati panu, ndi Mulungu wansanje ndipo adzakukwiyirani kwambiri ndi kukuwonongani, kukufafanizani mʼdziko. 16 Musamuyese Yehova Mulungu wanu monga munachitira ku Masa. 17 Onetsetsani kuti mukusunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, malangizo ake ndi zikhazikitso zake zimene anakulamulirani. 18 Chitani zoyenera ndi zabwino pamaso pa Yehova, kuti zikuyendereni bwino ndi kuti mukhoza kukalowa ndi kulanda dziko labwinolo limene Yehova analonjeza molumbira kwa makolo anu, 19 kupirikitsiratu adani anu onse, monga Yehova wanenera.
20 Mʼtsogolo muno, ana anu akadzakufunsani kuti, “Kodi tanthauzo la ndondomeko, malangizo, zikhazikitso ndi malamulo amene Yehova Mulungu wathu anakulamulani nʼchiyani?” 21 Inu mudzawawuze kuti, “Ife tinali akapolo a Farao ku Igupto, koma Yehova anatitulutsa ku Igupto ndi dzanja lamphamvu. 22 Ifeyo tikuona Yehova anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa, zazikulu ndi zoopsa, pa Aigupto ndi Farao pamodzi ndi banja lake lonse. 23 Koma anatitulutsa kumeneko ndi kutilowetsa kuno natipatsa dziko limene analonjeza mwa lumbiro kwa makolo athu. 24 Yehova anatilamula kuti tizimvera malamulo onsewa, kuti tizimuopa kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu monga momwe zilili leromu. 25 Ndipo ngati tisamala kumvera malamulo onsewa pamaso pa Yehova Mulungu wathu monga momwe anatilamulira ife, chimenecho chidzakhala chilungamo chathu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.