Deuteronomo 27
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Guwa Lansembe ku Phiri la Ebala
27 Mose ndi akuluakulu a Israeli analamula anthu kuti, “Sungani malamulo onse amene ndikukupatsani lero lino. 2 Mukawoloka mtsinje wa Yorodani kulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, muyimiritse miyala ingapo ikuluikulu ndi kuyikulungiza. 3 Mulembepo mawu onse a malamulo amenewa pamene muwoloka kulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani. 4 Ndipo mukawoloka Yorodani muyimike miyala iyi pa Phiri la Ebala monga momwe ndikukulamulirani lero lino ndipo muyikulungize. 5 Pamenepo mumange guwa lansembe la miyala la Yehova Mulungu wanu. Musagwiritse ntchito chida chilichonse chachitsulo pa miyalapo. 6 Mumange guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu ndi miyala yakutchire ndi kuperekerapo nsembe yopsereza kwa Yehova Mulungu wanu. 7 Muperekerepo nsembe zopereka za chiyanjano, muzidye ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 8 Ndipo pa miyalapo mudzalembepo mawu onse a malamulo ndi malemba akuluakulu.”
Matemberero Kuchokera ku Phiri la Ebala
9 Kenaka Mose ndi ansembe, amene ndi Alevi anati kwa Aisraeli onse, “Khalani chete Aisraeli inu ndipo mumvetsere! Tsopano inu ndinu anthu a Yehova Mulungu wanu. 10 Muzimvera Yehova Mulungu wanu ndi kutsata malamulo ake ndi malangizo ake omwe ndikukupatsani lero lino.”
11 Tsiku lomwelo Mose analamula anthu kuti:
12 Mukawoloka Yorodani, mafuko awa akayimirire pa Phiri la Gerizimu ndi kudalitsa anthu: Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Yosefe ndi Benjamini. 13 Ndipo mafuko awa akayimirire pa Phiri la Ebala ndi kutchula matemberero: Rubeni, Gadi, Aseri, Zebuloni, Dani ndi Nafutali.
14 Alevi adzayankhula mokweza kwa Aisraeli onse kuti:
15 “Ndi wotembereredwa munthu amene asema chifanizo kapena kupanga fano, ndi kuchiyika mobisa, pakuti chimenechi ndi chinthu chodetsedwa pamaso pa Yehova, ntchito za manja a anthu.”
Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”
16 “Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira ulemu abambo ake kapena amayi ake.”
Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”
17 “Ndi wotembereredwa munthu amene amasuntha mwala wa malire wa mnzake.”
Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”
18 “Ndi wotembereredwa munthu amene amasocheretsa munthu wosaona pa msewu.”
Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”
19 “Ndi wotembereredwa munthu amene sachitira chilungamo mlendo, ana amasiye kapena mkazi wamasiye.”
Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”
20 “Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mkazi wa abambo ake pakuti iye sachitira ulemu pogona pa abambo ake.”
Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”
21 “Ndi wotembereredwa munthu amene achita chigololo ndi nyama ya mtundu uli wonse.”
Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”
22 “Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake kapena mwana wamkazi wa amayi ake.”
Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”
23 “Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi apongozi ake.”
Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”
24 “Ndi wotembereredwa munthu amene apha mnzake mwachinsinsi.”
Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”
25 “Ndi wotembereredwa munthu amene alandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.”
Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”
26 “Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita kapena sasunga mawu a malamulo awa.”
Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.