Amosi 6
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Tsoka kwa Osalabadira Kanthu
6 Tsoka kwa amene simukulabadira kanthu ku Ziyoni,
ndiponso kwa inu amene mukukhala mwamtendere pa Phiri la Samariya,
inu anthu otchuka ochokera ku mtundu wa anthu omveka,
kumene Aisraeli amafikako!
2 Pitani ku mzinda wa Kaline mukawuyangʼane;
mukapitenso ku Hamati-raba mzinda waukulu uja,
ndipo mukatsikirenso ku Gati kwa Afilisti.
Kodi mizinda imeneyi ndi yopambana maufumu anu awiriwa?
Kodi dziko lawo ndi lalikulu kupambana lanu?
3 Inu simulabadirako kuti tsiku loyipa lidzafika,
zochita zanu zimafulumizitsa ulamuliro wankhanza.
4 Mumagona pa mabedi owakongoletsa ndi minyanga ya njovu,
mumagona pa mipando yanu ya wofuwofu.
Mumadya ana ankhosa onona
ndi ana angʼombe onenepa.
5 Mumayimba azeze anu ndi kumangopeka
nyimbo pa zingʼwenyengʼwenye ngati Davide.
6 Mumamwera vinyo mʼzipanda zodzaza
ndipo mumadzola mafuta abwino kwambiri,
koma simumva chisoni ndi kuwonongeka kwa Yosefe.
7 Nʼchifukwa chake inu mudzakhala mʼgulu la anthu oyamba kupita ku ukapolo;
maphwando ndi zikondwerero zanu zidzatheratu.
Yehova Amanyansidwa ndi Kunyada kwa Israeli
8 Ambuye Yehova walumbira mʼdzina lake. Yehova Mulungu Wamphamvuzonse walengeza kuti,
“Ndimanyansidwa ndi kunyada kwa Yakobo,
ndimadana ndi nyumba zake zaufumu;
Ine ndidzawupereka mzindawu
pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo.”
9 Ngati anthu khumi otsala adzabisala mʼnyumba imodzi, nawonso adzafa ndithu. 10 Ndipo ngati mʼbale wake wa wina wakufayo, woyenera kusamala za maliro, adzafika kudzatulutsa mitembo mʼnyumbamo nʼkufunsa aliyense amene akubisalabe mʼnyumbamo kuti, “Kodi uli ndi wina wamoyo mʼmenemo?” Ndipo munthu wobisalayo ndi kuyankha kuti, “Ayi,” mʼbaleyo adzanena kuti, “Khala chete! Ife tisayerekeze kutchula dzina la Yehova.”
11 Pakuti Yehova walamula kuti
nyumba zikuluzikulu Iye adzazigamulagamula,
ndipo nyumba zazingʼono zidzasanduka maduka okhaokha.
12 Kodi akavalo amathamanga pa thanthwe?
Kodi wina amatipula ndi ngʼombe mʼnyanja?
Koma chiweruzo cholungama mwachisandutsa kukhala zinthu zakupha
ndipo chipatso cha chilungamo mwachisandutsa kukhala chowawa.
13 Inu amene mukunyadira kuti munagonjetsa Lo Debara
ndipo mukunena kuti, “Kodi sitinatenge Karinaimu ndi mphamvu zathu zokha?”
14 Koma Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akulengeza kuti,
“Inu nyumba ya Israeli, ndidzakudzutsirani mtundu wina wa anthu
umene udzakuzunzani
kuchokera ku Lebo Hamati mpaka ku Chigwa cha Araba.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.