Amosi 1
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
1 Mawu a Amosi, mmodzi mwa anthu oweta nkhosa ku Tekowa. Zimene iye anaona mʼmasomphenya zokhudza Israeli patatsala zaka ziwiri kuti chivomerezi chichitike, nthawi imene Uziya anali mfumu ya Yuda ndipo Yeroboamu mwana wa Yowasi anali mfumu ya Israeli.
2 Amosi anati:
“Yehova akubangula mu Ziyoni
ndipo akumveka ngati bingu mu Yerusalemu;
msipu wa abusa ukulira,
ndipo pamwamba pa Karimeli pakuwuma.”
Chiweruzo pa Anthu Oyandikana ndi Israeli
3 Yehova akuti,
“Chifukwa anthu a ku Damasiko akunka nachimwirachimwira,
Ine sindileka kuwalanga.
Popeza anapuntha Giliyadi
ndi zopunthira za mano achitsulo,
4 Ine ndidzatumiza moto pa nyumba ya Hazaeli
umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.
5 Ndidzathyola chipata cha Damasiko;
ndidzawononga mfumu yokhala ku Chigwa cha Aveni,
ndiponso iye amene akugwira ndodo yaufumu mu Beti-Edeni.
Anthu a ku Aramu adzapita ku ukapolo ku Kiri,”
akutero Yehova.
6 Yehova akuti,
“Chifukwa anthu a ku Gaza akunka nachimwirachimwira,
Ine sindileka kuwalanga.
Popeza anatenga ukapolo mtundu wathunthu
ndi kuwugulitsa ku Edomu,
7 ndidzatumiza moto pa makoma a Gaza
umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.
8 Ndidzawononga mfumu ya ku Asidodi
komanso amene akugwira ndodo yaufumu ku Asikeloni.
Ndidzalanga Ekroni,
mpaka wotsala mwa Afilisti atafa,”
akutero Ambuye Yehova.
9 Yehova akuti,
“Chifukwa anthu a ku Turo akunka nachimwirachimwira,
Ine sindileka kuwalanga.
Popeza iwo anagulitsa mtundu wathunthu ku ukapolo ku Edomu,
osasunga pangano laubale lija,
10 Ine ndidzatumiza moto pa makoma a Turo
umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.”
11 Yehova akuti,
“Chifukwa anthu a ku Edomu akunka nachimwirachimwira,
Ine sindileka kuwalanga.
Popeza anathamangitsa mʼbale wake ndi lupanga,
popanda nʼchifundo chomwe.
Popeza mkwiyo wake unakulabe
ndipo ukali wake sunatonthozeke,
12 Ine ndidzatumiza moto pa Temani
umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za Bozira.”
13 Yehova akuti,
“Chifukwa anthu a ku Amoni akunka nachimwirachimwira,
Ine sindileka kuwalanga.
Popeza anatumbula akazi oyembekezera a ku Giliyadi
nʼcholinga choti akuze malire awo,
14 Ine ndidzayatsa moto pa makoma a ku Raba
umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.
Padzakhala kulira kwakukulu pa tsiku la nkhondoyo,
kumenyana kudzakhala kwafumbi ngati mkuntho wa kamvuluvulu.
15 Mfumu yawo idzatengedwa kupita ku ukapolo,
iyo pamodzi ndi akuluakulu ake,”
akutero Yehova.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.