2 Akorinto 12
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Masomphenya a Paulo ndi Minga ya Mʼthupi Mwake
12 Ndiyenera kupitiriza kudzitamandira. Ngakhale palibe choti ndipindule, ndipitiriza kufotokoza za masomphenya ndi mavumbulutso ochokera kwa Ambuye. 2 Ndikudziwa munthu mwa Khristu amene zaka khumi ndi zinayi zapitazo anatengedwa kupita kumwamba kwachitatu. Sindikudziwa ngati zinachitika ali mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu. 3 Ndipo ndikumudziwa munthu ameneyu. Sindikudziwa ngati zinachitika mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu. 4 Munthuyu anatengedwa kupita ku paradizo. Ndipo anamva zinthu zosatheka kuneneka, zinthu zimene munthu saloledwa kunena. 5 Ndidzatamanda za munthu ngati ameneyu, koma sindidzadzitamandira ine mwini kupatula za kufowoka kwanga. 6 Ngakhale nditafuna kudzitamandira, sindingakhale chitsiru, chifukwa ndikunena zoona. Koma ndimapewa kuti pasapezeke munthu wondiganizira moposera chimene ndili chifukwa cha zimene ndimachita kapena kuyankhula, 7 kapena chifukwa cha mavumbulutso aakulu kuposa awa. Choncho, kuti ndisadzitukumule, ndinayikidwa minga mʼthupi langa, wamthenga wa Satana, kuti adzindizunza. 8 Katatu konse ndinapempha Ambuye kuti andichotsere. 9 Koma anandiwuza kuti, “Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka.” Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine. 10 Tsono, chifukwa cha Khristu, ndimakondwera pamene ndili wofowoka, pamene akundinyoza, pamene ndikumva zowawa, ndi pamene akundizunza ndi kundisautsa. Pakuti pamene ndili wofowoka ndiye kuti ndili wamphamvu.
Paulo Akhudzidwa ndi Akorinto
11 Ndadzisandutsa wopusa, koma inu mwandichititsa zimenezi. Ndinu amene munayenera kundichitira umboni. Ngakhale kuti sindine kanthu, koma sindine wochepetsetsa kwa “atumwi apamwamba” aja. 12 Ndinapirira pokuonetserani zizindikiro za mtumwi weniweni, pochita pakati panu zizindikiro, zodabwitsa ndi ntchito zamphamvu. 13 Kodi inu munaoneka ochepa motani ku mipingo ina, kupatula kuti sindinali cholemetsa kwa inu? Mundikhululukire cholakwa chimenechi!
14 Ndakonzeka tsopano kudzakuyenderani kachitatu, ndipo sindidzakhala cholemetsa kwa inu chifukwa ndikungofuna inuyo osati zinthu zanu. Pakuti ana sasamalira makolo koma makolo ndiwo asamalira ana. 15 Motero ndidzakondwera kukupatsani zanga zonse zimene ndili nazo ndi kudziperekanso ine mwini chifukwa cha inu. Kodi ine ndikamakukondani kwambiri chotere, inuyo mudzandikonda pangʼono? 16 Ena mwa inu amavomereza kuti sindinali cholemetsa. Komabe ena amaganiza kuti ndine wochenjera, ndipo ndinakuchenjererani. 17 Kodi ndinakudyerani masuku pamutu kudzera mwa wina aliyense amene ndinamutumiza kwa inu? 18 Ndinamupempha Tito kuti abwere kwanuko ndipo ndinamutumiza pamodzi ndi mʼbale wathu. Kodi kapena Tito anakudyerani masuku pamutu? Kodi iye ndi ine sitinachite zinthu mofanana ndi Mzimu mmodzi yemweyo?
19 Kodi mukuyesa kuti nthawi yonseyi takhala tikudzitchinjiriza tokha? Takhala tikuyankhula pamaso pa Mulungu monga anthu amene ali mwa Khristu; ndipo abwenzi okondedwa, chilichonse chimene timachita ndi chofuna kukulimbikitsani. 20 Pakuti ndikuona kuti pamene ndibwera sindidzakupezani monga mmene ndikufunira kuti muzikhalira, ndipo simungadzandione monga mmene mukufunira kundionera. Ndikuopa kuti pangadzakhale mkangano, nsanje, kupserana mitima, kugawikana, ugogodi, miseche, kudzitukumula ndi chisokonezo. 21 Ndikuopa kuti pamene ndidzabwerenso, Mulungu adzandichepetsa pamaso panu, ndipo ndidzamva chisoni ndi ambiri amene anachimwa kale ndipo sanalape zonyansa, zachigololo ndi zilakolako zoyipa zimene anachita.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.