1 Yohane 2
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
2 Inu Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zimenezi kuti musachimwe. Koma wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, Yesu Khristu, Wolungamayo. 2 Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso machimo onse a dziko lapansi.
Chikondi ndi Chidani
3 Ife timatsimikiza kuti tikumudziwa ngati tikusunga malamulo ake. 4 Munthu akamanena kuti, “Ine ndimadziwa Mulungu,” koma samvera malamulo a Mulunguyo, ndi wabodza ameneyo ndipo mwa iye mulibe choonadi. 5 Koma munthu aliyense akamvera mawu ake, ndiye kuti chikondi cha Mulungu chafikadi penipeni mwa iyeyo. Pamenepo timatsimikizadi kuti tili mwa Iye. 6 Aliyense amene amati amakhala mwa Mulungu, ayenera kukhala moyo umene Yesu ankakhala.
7 Okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano koma lakale lomwe lija, limene munali nalo kuyambira pachiyambi. Lamulo la kalelo ndi mawu amene munawamva kale. 8 Komabe ndi lamulo latsopano limene ndikukulemberani. Choonadi chake chikuoneka mwa Yesu ndiponso mwa inu, chifukwa mdima ukutha ndipo kuwunika kwenikweni kwayamba kale kuwala.
9 Aliyense amene amati ali mʼkuwunika, koma nʼkumadana ndi mʼbale wake ali mu mdima. 10 Aliyense amene amakonda mʼbale wake amakhalanso mʼkuwunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa. 11 Koma aliyense wodana ndi mʼbale wake ali mu mdima ndipo akuyenda mu mdima. Iyeyo sakudziwa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa mʼmaso mwake.
12 Inu ana okondedwa, ndikukulemberani
popeza kuti machimo anu akhululukidwa chifukwa cha dzina la Yesu.
13 Inu abambo, ndikukulemberani
popeza kuti munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.
Inu anyamata, ndikukulemberani
popeza kuti munagonjetsa woyipayo.
14 Ana okondedwa, ndikukulemberani
chifukwa mumawadziwa Atate.
Abambo, ndikukulemberani
chifukwa munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.
Inu anyamata, ndikukulemberani
chifukwa ndinu amphamvu.
Mawu a Mulungu amakhala mwa inu
ndipo mumamugonjetsa woyipayo.
Musakonde Dziko Lapansi
15 Musamakonde dziko lapansi kapena chilichonse cha dziko lapansi. Ngati munthu wina aliyense akonda dziko lapansi, mwa iyeyo mulibe chikondi chokonda Atate. 16 Pakuti zonse za mʼdziko lapansi, zilakolako za thupi, zinthu zimene maso amakhumbira ndiponso kuyandikira zinthu za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. 17 Dziko lapansi likupita pamodzi ndi zilakolako zake, koma amene amachita chifuniro cha Mulungu amakhalapo mpaka muyaya.
Anthu Okana Khristu
18 Ana anga, ino ndi nthawi yotsiriza, ndipo monga munamva kale kuti anthu okana Khristu akubwera, ngakhale tsopano okana Khristu ambiri afika kale. Zimenezi zikutisonyeza kuti ino ndi nthawi yotsiriza. 19 Anthu amenewa anachoka pakati pathu, komatu sanali a mʼgulu lathu. Pakuti akanakhala a mʼgulu lathu, akanakhalabe nafe, koma kuchoka kwawo kunatisonyeza kuti sanali a mʼgulu lathu.
20 Koma inu muli ndi kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo nonsenu mukudziwa choonadi. 21 Sindikukulemberani chifukwa choti simudziwa choonadi ayi, koma chifukwa choti mumadziwa choonadicho, ndipo mukudziwanso kuti bodza silichokera pa choonadi. 22 Wabodzayo ndani? Ndi munthu aliyense amene amanena kuti Yesu si Mpulumutsi. Munthu woteroyo ndi wokana Khristu, ndiponso amakana Atate, ndi Mwana. 23 Aliyense wokana Mwana alibenso Atate. Wovomereza Mwana alinso ndi Atate.
24 Onetsetsani kuti zimene munazimva kuyambira pachiyambi zikhalebe mwa inu. Ngati zikhala mwa inu, inunso mudzakhala mwa Mwana ndiponso mwa Atate. 25 Ndipo chimene anatilonjeza nʼchimenechi: moyo wosatha.
26 Ine ndikukulemberani zimenezi kuti ndikuwuzeni za amene akufuna kukusocheretsani. 27 Koma za inu, kudzoza kumene munalandira kwa Khristu kuli mwa inu, ndipo sipafunika wina aliyense kuti akuphunzitseni. Koma kudzozako kumakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo popeza kudzoza kwakeko nʼkoona osati konama, monga munaphunzira, khalani mwa Iyeyo.
Ana a Mulungu
28 Tsopano ana okondedwa, khalani mwa Yesu, kuti pamene adzaonekera, ife tidzakhale otsimikizika mu mtima ndi wopanda manyazi pamaso pake akamadzabwera.
29 Popeza mukudziwa kuti Khristu ndi wolungama, choncho mukudziwanso kuti aliyense amene amachita chilungamo ndi mwana wa Mulungu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.