1 Samueli 29
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Afilisti Akana Davide
29 Afilisti anasonkhanitsa asilikali awo onse ku Afeki, ndipo Israeli anamanga misasa yawo pa chitsime cha Yezireeli. 2 Pamene atsogoleri a Afilisti ankatsogolera magulu awo ankhondo a miyandamiyanda, Davide ndi ankhondo ake ankayenda pambuyo pamodzi ndi Akisi. 3 Tsono atsogoleri a Afilisti aja anafunsa kuti, “Kodi Ahebri awa akufuna chiyani?”
Akisi anayankha kuti, “Uyu ndi Davide, mtumiki wa Sauli mfumu ya Israeli. Iye wakhala ndi ine kwa masiku ndithu, kapena titi zaka ndipo kuyambira tsiku limene anachoka kwa Sauli mpaka lero, ine sindinapeze cholakwa mwa iye.”
4 Koma atsogoleri a ankhondo a Afilisti anamukwiyira Akisi kwambiri ndipo anati, “Mubweze munthuyu kuti abwerere ku malo amene unamupatsa. Iye asapite nafe ku nkhondo kuopa kuti angadzasanduke mdani wathu. Kodi iyeyu adzadziyanjanitsa bwanji ndi mbuye wake? Iyeyutu adzadziyanjanitsa ndi mbuye wake pakupha anthu ali panowa? 5 Paja ameneyu ndi Davide yemwe ankamuvinira namuyimbira kuti,
“ ‘Sauli wapha anthu 1,000
koma Davide wapha miyandamiyanda?’ ”
6 Kotero Akisi anayitana Davide ndipo anamuwuza kuti, “Pali Yehova wamoyo, iwe wakhala wodalirika ndipo chikanakhala chinthu chabwino kuti uzimenya nkhondo pamodzi nane popeza chibwerere iwe kuno ine sindinapeze cholakwa chilichonse ndi iwe. Koma atsogoleri enawa ndiwo sakukufuna. 7 Tsono bwerera. Upite mu mtendere kuopa kuti ungachite kanthu kena koyipira atsogoleri a Afilistiwa.”
8 Davide anafunsa Akisi kuti, “Kodi ndachita chiyani? Kodi mwapeza cholakwa chotani mwa ine mtumiki wanu chiyambire kukutumikirani mpaka lero? Tsono chifukwa chiyani sindingapite kukamenya nkhondo ndi adani a mbuye wanga mfumu?”
9 Akisi anayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti ndiwe wangwiro ngati mngelo wa Mulungu. Komabe atsogoleri a ankhondo a Afilisti akuti, ‘Davide asapite nafe ku nkhondo.’ 10 Tsono udzuke mmamawa, pamodzi ndi ankhondo ako amene unabwera nawo, ndipo unyamuke kukangocha.”
11 Choncho Davide ndi anthu ake anadzuka mmamawa kubwerera ku dziko la Afilisti. Koma Afilistiwo anapita ku Yezireeli.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.